Hoseya 7:2 - Buku Lopatulika Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukira zoipa zao zonse; tsopano machitidwe ao awazinga; ali pamaso panga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukira zoipa zao zonse; tsopano machitidwe ao awazinga; ali pamaso panga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma saganiza kuti Ine sindiiŵala ntchito zao zoipa. Zolakwa zao zaŵazinga, ndipo sizichoka m'maso mwanga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma sazindikira kuti Ine ndimakumbukira zoyipa zawo zonse. Azunguliridwa ndi zolakwa zawo; ndipo sizichoka mʼmaso mwanga. |
Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.
Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.
Ng'ombe idziwa mwini wake, ndi bulu adziwa pomtsekereza: koma Israele sadziwa, anthu anga sazindikira.
Palibe wina wokumbukira, kapena kudziwa, kapena kuzindikira, ndi kuti, Ndatentha mbali ina pamoto, inde ndaotchanso mkate pamakala pake, ndakazinga nyama ndi kuidya; kodi ndichipange chotsala chake, chikhale chonyansa? Ndidzagwadira kodi tsinde la mtengo?
Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m'maphwando ao; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa machitidwe a manja ake.
Atero Yehova kwa anthu awa, Chomwecho akonda kusocherera; sanakanize mapazi ao; chifukwa chake Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira choipa chao, nadzalanga zochimwa zao.
Pakuti maso anga ali panjira zao zonse, sabisika pa nkhope yanga, mphulupulu yao siibisika pamaso panga.
Tchimo la Yuda lalembedwa ndi peni lachitsulo, ndi nsonga ya diamondi; lalembedwa pa cholembapo cha m'mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe ao.
Choipa chako chidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu.
wamkulu mu upo, wamphamvu m'ntchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa chipatso cha machitidwe ake;
Njira yako ndi ntchito zako zinakuchitira izi; ichi ndicho choipa chako ndithu; chili chowawa ndithu, chifikira kumtima wako.
Zofukizira zanu m'mizinda ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, za inu ndi atate anu, mafumu anu ndi akulu anu, ndi anthu a m'dziko, kodi Yehova sanazikumbukire, kodi sizinalowe m'mtima mwake?
Akuonera zopanda pake, akuombezera mabodza, lupanga likugoneka pa makosi a oipa olasidwa, amene lafika tsiku lao nthawi ya mphulupulu yotsiriza.
Ndipo Yehova ali ndi mlandu ndi Yuda, nadzalanga Yakobo monga mwa njira zake, adzambwezera monga mwa machitidwe ake.
Ndipo kudzakhala monga anthu, momwemo wansembe; ndipo ndidzawalanga chifukwa chanjira zao, ndi kuwabwezera machitidwe ao.
Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake.
Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukira mphulupulu yao, nadzalanga zochimwa zao; adzabwerera kunka ku Ejipito.
Choipa chao chonse chili mu Giligala; pakuti pamenepo ndinawada, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe ao ndidzawainga kuwachotsa m'nyumba mwanga; sindidzawakondanso; akalonga ao onse ndiwo opanduka.
Anadzivunditsa kwambiri, monga masiku a Gibea; adzakumbukira mphulupulu yao, adzalanga zochimwa zao.
Yehova walumbira pali kudzikuza kwa Yakobo, Ngati ndidzaiwala konse ntchito zao zilizonse?
Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukuluwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti choipa chao chandikwerera pamaso panga.
Koma mukapanda kutero, taonani, mwachimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti tchimo lanu lidzakupezani.
Koma kulibe kanthu kovundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika.
Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.
Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.