Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Hoseya 9:15 - Buku Lopatulika

15 Choipa chao chonse chili mu Giligala; pakuti pamenepo ndinawada, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe ao ndidzawainga kuwachotsa m'nyumba mwanga; sindidzawakondanso; akalonga ao onse ndiwo opanduka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Choipa chao chonse chili m'Giligala; pakuti pamenepo ndinawada, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe ao ndidzawainga kuwachotsa m'nyumba mwanga; sindidzawakondanso; akalonga ao onse ndiwo opanduka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Chauta akuti, “Kuipa kwao konse kudaoneka makamaka ku Giligala. Ndidayamba kudana nawo kumeneko. Ndidzaŵapirikitsa m'dziko mwanga, chifukwa makhalidwe ao ndi oipa. Sindidzaŵakondanso, atsogoleri ao onse andiwukira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 “Chifukwa cha zoyipa zawo zonse ku Giligala, Ine ndinawada kumeneko. Chifukwa cha machitidwe awo auchimo, ndidzawapirikitsa mʼnyumba yanga. Sindidzawakondanso; atsogoleri awo onse ndi owukira.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 9:15
38 Mawu Ofanana  

ndipo anachokera chokhalamo cha ku Silo, chihemacho adachimanga mwa anthu;


Akulu ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera milandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.


Wokondedwa wanga afunanji m'nyumba mwanga, popeza wachita choipa ndi ambiri, ndipo thupi lopatulika lakuchokera iwe? Pamene uchita choipa ukondwera nacho.


Cholowa changa chandisandukira mkango wa m'nkhalango; anatsutsana nane ndi mau ake; chifukwa chake ndinamuda.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Ndipo ndinaona, kuti, ndingakhale ndikamchotsa Israele wobwerera m'mbuyo, ndi kumpatsa kalata yachilekaniro chifukwa cha kuchita chigololo iye, mphwake Yuda wonyenga sanaope, koma iye yemwe ananka nachita dama.


Ine ndidzanka kwa akulu, ndidzanena ndi iwo; pakuti adziwa njira ya Yehova, ndi chiweruzo cha Mulungu wao. Koma awa anavomerezana nathyola goli, nadula zomangira zao.


Akalonga ake m'kati mwake akunga mimbulu yakumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuononga miyoyo, kuti aone phindu lonyenga.


M'mwemo iye anawulula chigololo chake, navula umaliseche wake; pamenepo moyo wanga unaipidwa naye, monga umo moyo unaipidwira mkulu wake.


Ndipo anaimanso, nabala mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Wosachitidwa-chifundo; pakuti sindidzachitiranso chifundo nyumba ya Israele, kuti ndiwakhululukire konse.


Ndipo Yehova anati, Umutche dzina lake Si-anthu-anga; pakuti inu sindinu anthu anga, ndipo Ine sindine wanu.


Kodi Giliyadi ndiye wopanda pake? Akhala achabe konse; mu Giligala aphera nsembe ya ng'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'michera ya munda.


Ndipo Yehova ali ndi mlandu ndi Yuda, nadzalanga Yakobo monga mwa njira zake, adzambwezera monga mwa machitidwe ake.


Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;


Chinkana iwe, Israele, uchita uhule, koma asapalamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.


Ndipo kudzakhala monga anthu, momwemo wansembe; ndipo ndidzawalanga chifukwa chanjira zao, ndi kuwabwezera machitidwe ao.


Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukira zoipa zao zonse; tsopano machitidwe ao awazinga; ali pamaso panga.


Mulungu wanga adzawataya, pakuti sanammvere Iye; ndipo adzakhala othawathawa mwa amitundu.


Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efuremu adzabwerera kunka ku Ejipito; ndipo adzadya chakudya chodetsa mu Asiriya.


Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu.


Idzani ku Betele, mudzalakwe ku Giligala, nimuchulukitse zolakwa, nimubwere nazo nsembe zanu zophera m'mawa ndi m'mawa, magawo anu akhumi atapita masiku atatuatatu;


M'mwemo ndidzakutengani kunka nanu kundende kutsogolo kwa Damasiko, ati Yehova, amene dzina lake ndiye Mulungu wa makamu.


koma musamafuna Betele, kapena kumalowa mu Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe.


Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera.


Anthu anga, kumbukiranitu chofunsira Balaki mfumu ya Mowabu, ndi chomuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova.


Akalonga ake m'kati mwake ndiwo mikango yobangula; oweruza ake ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.


Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane.


Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mzinda muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza;


Ndipo atamva ichi, analowa mu Kachisi mbandakucha, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene anali naye, nasonkhanitsa a bwalo la akulu a milandu, ndi akulu onse a ana a Israele, natuma kundende atengedwe ajawo.


Pamenepo Yoswa ndi Aisraele onse naye, anabwerera kuchigono ku Giligala.


Ndipo anayenda chozungulira chaka ndi chaka ku Betele, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israele m'malo onse amenewa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa