Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 17:1 - Buku Lopatulika

1 Tchimo la Yuda lalembedwa ndi peni lachitsulo, ndi nsonga ya diamondi; lalembedwa pa cholembapo cha m'mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Tchimo la Yuda lalembedwa ndi peni lachitsulo, ndi nsonga ya diamondi; lalembedwa pa cholembapo cha m'mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta akuti, “Uchimo wa Yuda ndi wolembedwa ndi cholembera chachitsulo, cha nsonga ya mwala wadaimondi. Uchimowo walembedwa pa mitima yao ndiponso pa maguwa ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Tchimo la Yuda lazokotedwa ndi cholembera cha chitsulo, lalembedwa ndi msonga ya mwala wadayimondi. Uchimowo walembedwa pa mitima yawo ndiponso pa nyanga za maguwa awo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 17:1
15 Mawu Ofanana  

Chifundo ndi choonadi zisakusiye; uzimange pakhosi pako; uzilembe pamtima pako;


Uwamange pa zala zako, uwalembe pamtima pako.


Taona ndakulembera iwe pa zikhato za manja anga; makoma ako alipo masiku onse pamaso panga.


Pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa mizinda yako, iwe Yuda; ndi maguwa a nsembe amene mwautsira chamanyazi, alingana ndi kuchuluka kwa miseu ya Yerusalemu, ndiwo maguwa akufukizirapo Baala.


Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu.


Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;


Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati?


Kodi Giliyadi ndiye wopanda pake? Akhala achabe konse; mu Giligala aphera nsembe ya ng'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'michera ya munda.


Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukira zoipa zao zonse; tsopano machitidwe ao awazinga; ali pamaso panga.


Popeza Efuremu anachulukitsa maguwa a nsembe akuchimwako, maguwa a nsembe omwewo anamchimwitsa.


Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake patsinde pa guwa la nsembe yopsereza.


Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwaa, kuti angamve chilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wake mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukulu wochokera kwa Yehova wa makamu.


popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata ya Khristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa