Numeri 32:23 - Buku Lopatulika23 Koma mukapanda kutero, taonani, mwachimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti tchimo lanu lidzakupezani. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 Koma mukapanda kutero, taonani, mwachimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti tchimo lanu lidzakupezani. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa23 Koma ngati simuchita choncho, mwachimwira Chauta, ndipo dziŵani kuti tchimo lanu lidzakutsatani. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 “Koma mukalephera kuchita izi, mudzakhala mukuchimwira Yehova. Ndipo dziwani kuti tchimo lanu lidzakupezani. Onani mutuwo |
Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.