Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 50:22 - Buku Lopatulika

22 Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 “Ganizani bwino izi tsono, inu amene mumaiŵala Mulungu, kuti ndingakukadzuleni, ndipo palibe amene angakupulumutseni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 “Ganizira izi, iwe amene umayiwala Mulungu kuti ndingakukadzule popanda wokupulumutsa:

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 50:22
21 Mawu Ofanana  

Anayang'ana iwo, koma panalibe wopulumutsa; ngakhale kwa Yehova, koma Iye sanawayankhe.


chinkana mudziwa kuti sindili woipa, ndipo palibe wakupulumutsa m'dzanja lanu?


Momwemo mayendedwe a onse oiwala Mulungu; ndi chiyembekezo cha onyoza Mulungu; chidzatayika.


Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.


kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango, ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa.


Oipawo adzabwerera kumanda, inde amitundu onse akuiwala Mulungu.


Pakuti sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi, kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzaonongeka kosatha.


Tsiku la mwai kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ichi pambali pa chinzake, kuti anthu asapeze kanthu ka m'tsogolo mwao.


waiwala Yehova Mlengi wako, amene anayala m'mwamba, nakhazika maziko a dziko lapansi, ndi kuopabe tsiku lonse chifukwa cha ukali wa wotsendereza, pamene iye akonzeratu kupasula? Uli kuti ukali wa wotsendereza?


Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwatibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.


Popeza anasamalira, natembenukira kuleka zolakwa zake zonse adazichita, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.


Ndidzakomana nao ngati chimbalangondo chochilanda ana ake, ndi kung'amba chokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; chilombo chidzawamwetula.


Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala chilamulo cha Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.


Pakuti ndidzakhala kwa Efuremu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kuchoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa.


Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yake, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wake;


Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.


Chifukwa chake tsono, atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu.


Koma m'mene anakumbukira mumtima, anati, Antchito olipidwa ambiri a atate wanga ali nacho chakudya chochuluka, ndipo ine ndionongeke kuno ndi njala?


Mwaleka Thanthwe limene linakubalani, mwaiwala Mulungu amene anakulengani.


Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa