Hoseya 7:1 - Buku Lopatulika1 M'mene ndichiritsa Israele, mphulupulu ya Efuremu ivumbuluka, ndi zoipa za Samariya; pakuti achita bodza, ndipo mkhungu alowa m'nyumba, ndi gulu la mbala lilanda kubwalo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 M'mene ndichiritsa Israele, mphulupulu ya Efuremu ivumbuluka, ndi zoipa za Samariya; pakuti achita bodza, ndipo mkhungu alowa m'nyumba, ndi gulu la mbala lilanda kubwalo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Ndikati ndibwezere anthu anga pabwino, ndikati ndichiritse Aisraele, uchimo wao umaonekera poyera. Ntchito zoipa za anthu a ku Samariyawo sizibisika ai. Sakhulupirika, amanyenga anthu, amathyola nyumba ngati mbala, ndi achifwamba, amalandanso zinthu za anthu poyera. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Pamene ndichiritsa Israeli, machimo a Efereimu amaonekera poyera ndiponso milandu ya Samariya sibisika. Iwo amachita zachinyengo, mbala zimathyola nyumba, achifwamba amalanda anthu katundu mʼmisewu. Onani mutuwo |