Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 90:8 - Buku Lopatulika

8 Munaika mphulupulu zathu pamaso panu, ndi zoipa zathu zobisika pounikira nkhope yanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Munaika mphulupulu zathu pamaso panu, ndi zoipa zathu zobisika pounikira nkhope yanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Inu mwaika machimo athu pamaso panu, ngakhale machimo obisika mwaŵaonetsa poyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mwayika mphulupulu zathu pamaso panu, machimo athu obisika poonekera pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 90:8
23 Mawu Ofanana  

Ndikachimwa mundipenya; ndipo simudzandimasula mphulupulu yanga.


Pakuti maso ake ali panjira ya munthu aliyense, napenya moponda mwake monse.


Anena m'mtima mwake, Mulungu waiwala; wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse.


Zikhale pamaso pa Yehova chikhalire, kuti adule chikumbukiro chao kuchichotsera kudziko lapansi.


Adziwitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika.


Izi unazichita iwe, ndipo ndinakhala chete Ine; unayesa kuti ndifanana nawe, ndidzakudzudzula, ndi kuchilongosola pamaso pako.


Unapserera ndi moto, unadulidwa; aonongeka pa kudzudzula kwa nkhope yanu.


Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova, asinkhasinkha za mayendedwe ake onse.


Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.


Pakuti maso anga ali panjira zao zonse, sabisika pa nkhope yanga, mphulupulu yao siibisika pamaso panga.


Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu.


Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.


Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m'chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.


akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake, ndicho tonde wopanda chilema;


akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake mbuzi yaikazi, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita.


tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Khristu Yesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino.


Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


m'mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.


Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aang'ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa ntchito zao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa