Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 90:7 - Buku Lopatulika

7 Pakuti tionongeka mu mkwiyo wanu; ndipo m'kuzaza kwanu tiopsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Pakuti tionongeka mu mkwiyo wanu; ndipo m'kuzaza kwanu tiopsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ife tapseratu ndi mkwiyo wanu woyaka, tikufa ndi mantha chifukwa cha ukali wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ife tathedwa ndi mkwiyo wanu; ndipo taopsezedwa ndi kuyipidwa kwanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 90:7
13 Mawu Ofanana  

Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu, mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete. Indedi, munthu aliyense ali chabe.


Muwathe mumkwiyo, muwagulule psiti. Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza mu Yakobo, kufikira malekezero a dziko la pansi.


Potero anathera masiku ao ndi zopanda pake, ndi zaka zao mwa mantha.


Adziwa mphamvu ya mkwiyo wanu ndani, ndi ukali wanu monga ayenera kukuopani?


Pakuti masiku athu onse apitirira mu ukali wanu; titsiriza moyo wathu ngati lingaliro.


Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m'moto ndi m'mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aejipito, nauvuta ulendo wa Aejipito.


Munaponda dziko ndi kulunda, munapuntha amitundu ndi mkwiyo.


Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m'chipululu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa