Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 9:16 - Buku Lopatulika

16 Anadziwika Yehova, anachita kuweruza, woipayo anakodwa ndi ntchito ya manja ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Anadziwika Yehova, anachita kuweruza, woipayo anakodwa ndi ntchito ya manja ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Chauta wadziwulula yekha, pakuweruza molungama, koma anthu oipa akodwa mu msampha wotcha iwo omwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Yehova amadziwika ndi chilungamo chake; oyipa akodwa ndi ntchito za manja awo. Higayoni. Sela

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 9:16
26 Mawu Ofanana  

Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m'dzanja lake, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokhanokha.


Msampha udzamgwira kuchitendeni, ndi khwekhwe lidzamkola.


Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao.


Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga, choipa cha milomo yao chiwaphimbe.


Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.


Likondwere phiri la Ziyoni, asekere ana aakazi a Yuda, chifukwa cha maweruzo anu.


Mverani mau anga, Yehova, Zindikirani kulingirira kwanga.


Chovuta chake chidzambwerera mwini, ndi chiwawa chake chidzamgwera pakati pamutu pake.


Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa; pazeze ndi kulira kwake.


Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israele anatukula maso ao, taonani, Aejipito alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israele anafuulira kwa Yehova.


Ndipo Israele anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aejipito, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.


Ndipo ndidzalimbitsa mtima wake wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yake yonse; pamenepo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndipo anachita chomwecho.


Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aejipito, ndikutulutsa ana a Israele pakati pao.


M'kulakwa kwa milomo muli msampha woipa; koma wolungama amatuluka m'mavuto.


wakodwa ndi mau a m'kamwa mwako, wagwidwa ndi mau a m'kamwa mwako.


Chifukwa chake mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa chambuyo, ndi kuthyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa.


Ndipo ambiri adzaphunthwapo, nagwa, nathyoka, nakodwa, natengedwa.


Pamenepo mfumu Dariusi analembera kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe onse okhala padziko lonse lapansi, Mtendere uchulukire inu.


Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.


Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa