Masalimo 9:15 - Buku Lopatulika15 Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba, lakodwa phazi lao muukonde anautchera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba, lakodwa phazi lao muukonde anautcha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Akunja agwera m'mbuna yokumba iwo omwe. Phazi lao lakodwa mu ukonde wobisika wotcha iwo omwe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Mitundu ya anthu yagwa mʼdzenje limene yakumba; mapazi awo akodwa mu ukonde umene anawubisa. Onani mutuwo |