Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.
Genesis 17:8 - Buku Lopatulika Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Dziko lino limene ukukhalamo ngati mlendoli, ndidzakupatsa iwe ndi zidzukulu zako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala la zidzukulu zako mpaka muyaya, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dziko lonse la Kanaani, limene iwe ukukhala tsopano, ndalipereka kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako kuti likhale chuma chanu mpaka muyaya. Ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wa zidzukulu zako.” |
Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.
chifukwa kuti dziko lonse limene ulinkuona, ndidzakupatsa iwe ndi mbeu yako nthawi yonse.
Tauka, nuyendeyende m'dzikoli m'litali mwake ndi m'mimba mwake; chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo.
Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.
Ndipo Yehova anamuonekera iye usiku womwewo, nati, Ine ndine Mulungu wa Abrahamu atate wako; usaope, chifukwa kuti Ine ndili ndi iwe, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kuchulukitsa mbeu zako, chifukwa cha Abrahamu kapolo wanga.
akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu.
Ndipo Yakobo anafika kwa Isaki atate wake ku Mamure, ku Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni) kumene anakhala Abrahamu ndi Isaki.
Chifukwa chuma chao chinali chambiri chotero kuti sanakhoze kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoze kuwakwanira chifukwa cha ng'ombe zao.
Taona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakuchulukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbeu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale laolao chikhalire.
Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu; koma Iye anapangana ndi ine pangano losatha, lolongosoka mwa zonse ndi losungika; pakuti ichi ndi chipulumutso changa chonse, ndi kufuma kwanga konse, kodi sadzachimeretsa?
Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;
Ndipo kudzakhala, atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, monga anakulumbirira iwe ndi makolo ako, ndipo anakupatsa ilo,
pamenepo mbuye wake azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wake am'boole khutu lake ndi lisungulo; ndipo iye azimgwirira ntchito masiku onse.
Kumbukirani Abrahamu, Isaki ndi Israele, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzitchula nokha, amene munanena nao, Ndidzachulukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale cholowa chao nthawi zonse.
nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andichitire ntchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao.
Ndipo ndinakhazikitsanso nao chipangano changa, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo ao, anali alendo m'mwemo.
ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakutulutsa inu pansi pa akatundu a Aejipito.
ndi kuti, Mubwerere tsopano nonsenu, yense kuleka njira yake yoipa, ndi zoipa za ntchito zanu, ndi kukhala m'dziko limene Yehova anapatsa inu ndi makolo anu, kuyambira kale kufikira muyaya;
Nthawi yomweyo, ati Yehova, ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Israele, ndipo iwo adzakhala anthu anga.
kuti ayende m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; ndipo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao.
Wobadwa ndi munthu iwe, iwo okhala kumabwinja a dziko la Israele anena, ndi kuti, Abrahamu anali yekha, nakhala nalo dziko cholowa chake; koma ife ndife ambiri, dzikoli lipatsidwa kwa ife cholowa chathu.
Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanulanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanulanu;
Ndipo ichi chikhale kwa inu lemba losatha, kuchita chotetezera ana a Israele, chifukwa cha zochimwa zao zonse, kamodzi chaka chimodzi. Ndipo anachita monga Yehova adauza Mose.
Ndipo ndidzayendayenda pakati pa inu, ndi kukhala Mulungu wanu ndi inu mudzakhala anthu anga.
ndipo ndidzabwera nao, nadzakhala m'kati mwa Yerusalemu; ndipo iwo adzakhala anthu anga, nanenanso ndidzakhala Mulungu wao, m'choonadi ndi m'chilungamo.
Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reuwele Mmidiyani mpongozi wa Mose, Ife tili kuyenda kunka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakuchitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israele zokoma.
ndipo lidzakhala kwa iye, ndi kwa mbeu zake zakumtsata pangano la unsembe wosatha, popeza anachita nsanje chifukwa cha Mulungu wake, anawachitira ana a Israele chowatetezera.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kwera m'phiri ili la Abarimu, nupenye dziko limene ndapatsa ana a Israele.
ndipo sanampatse cholowa chake m'menemo, ngakhale popondapo phazi lake iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lake, ndi la mbeu yake yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.
Popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope padziko lapansi.
Ndipo Yehova wakulonjezetsani lero kuti mudzakhala anthu akeake a pa okha, monga ananena ndi inu, ndi kuti mudzasunga malamulo ake onse;
kuti adzikhazikire inu, mtundu wake wa anthu lero lino, ndi kuti akhale kwa inu Mulungu, monga ananena ndi inu, ndi monga analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo.
Kwera m'phiri muno mwa Abarimu, phiri la Nebo, lokhala m'dziko la Mowabu, popenyana ndi Yeriko; nupenye dziko la Kanani, limene ndipereka kwa ana a Israele likhale laolao;
Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu cholowa chao, pamene anagawa ana a anthu, anaika malire a mitundu ya anthu, monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israele.
Ndipo Yehova anati kwa iye, Si ili dziko ndinalumbirira Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzalipereka kwa mbeu zako. Ndinakuonetsa ili m'maso, koma sudzaolokako.
Ndipo popeza anakonda makolo anu, anasankha mbeu zao zakuwatsata, nakutulutsani pamaso pake ndi mphamvu yake yaikulu, mu Ejipito;
Simulowa kulandira dziko lao chifukwa cha chilungamo chanu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.
Ndipo mwa ichi ali Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti, popeza kudachitika imfa yakuombola zolakwa za pa chipangano choyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha.
Mose mtumiki wanga wafa; tauka tsono, nuoloke Yordani uyu, iwe ndi anthu awa onse, kulowa m'dzikomo ndilikuwapatsa, ndiwo ana a Israele.
Iye wakupambana adzalandira izi; ndipo ndidzakhala Mulungu wake, ndi iye adzakhala mwana wanga.