Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 16:34 - Buku Lopatulika

34 Ndipo ichi chikhale kwa inu lemba losatha, kuchita chotetezera ana a Israele, chifukwa cha zochimwa zao zonse, kamodzi chaka chimodzi. Ndipo anachita monga Yehova adauza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Ndipo ichi chikhale kwa inu lemba losatha, kuchita chotetezera ana a Israele, chifukwa cha zochimwa zao zonse, kamodzi chaka chimodzi. Ndipo anachita monga Yehova adauza Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Limeneli lidzakhala lamulo lanu lamuyaya, kuti muzidzachita mwambo wopepesera machimo onse a Aisraele kamodzi pa chaka.” Tsono Mose adachita monga momwe Chauta adamlamulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 “Ili likhale lamulo lanu lamuyaya. Mwambo wopepesera machimo uzichitika kamodzi pa chaka chifukwa cha machimo a anthu onse.” Ndipo Mose anachita monga momwe Yehova analamulira.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 16:34
14 Mawu Ofanana  

Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.


Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova.


Ndipo Mose anaona ntchito zonse, ndipo, taonani, adaichita monga Yehova adamuuza, momwemo adachita. Ndipo Mose anawadalitsa.


ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Musamagwira ntchito iliyonse tsiku limenelo; pakuti ndilo tsiku la chitetezero, kuchita chotetezera inu pamaso pa Yehova Mulungu wanu.


Musamagwira ntchito iliyonse; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zonse.


Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, ndipo anatulutsa wotembererayo kunja kwa chigono, namponya miyala. Ndipo ana a Israele anachita monga Yehova adauza Mose.


Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.


Ndipo tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri uwu muzikhala nako kusonkhana kopatulika; pamenepo mudzichepetse, musamagwira ntchito;


Pakuti ndi chipereko chimodzi anawayesera angwiro chikhalire iwo oyeretsedwa.


Komatu mu izizo muli chikumbukiro cha machimo chaka ndi chaka.


kosati kuti adzipereke yekha kawirikawiri; monga mkulu wa ansembe alowa m'malo opatulika chaka ndi chaka ndi mwazi wosati wake;


koma kulowa m'chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa