Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 12:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Chauta adaonekera Abramu namuuza kuti, “Dziko limeneli ndidzapatsa zidzukulu zako.” Choncho pa malo amenewo Abramu adamanga guwa, kumangira Chauta amene adaamuwonekera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 12:7
55 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anachoka kumeneko kunka kuphiri la kum'mawa kwa Betele, namanga hema wake; Betele anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.


chifukwa kuti dziko lonse limene ulinkuona, ndidzakupatsa iwe ndi mbeu yako nthawi yonse.


Tauka, nuyendeyende m'dzikoli m'litali mwake ndi m'mimba mwake; chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo.


Ndipo Abramu anasuntha hema wake nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure, imene ili mu Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.


kumalo kwa guwa la nsembe analimanga iye kumeneko, poyamba paja; ndipo pamenepo Abramu anaitanira dzina la Yehova.


Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:


Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.


Ndipo Abramu anagwa nkhope pansi, ndipo Mulungu ananena naye kuti,


Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wako.


Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamure, pamene anakhala pa khomo la hema wake pakutentha dzuwa.


Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isaki mwana wake, namuika iye paguwa la nsembe pamwamba pa nkhuni.


Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine kunyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; Iye adzatumiza mthenga wake akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko.


Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, naitana dzina la Yehova, namanga hema wake kumeneko: ndi pamenepo anyamata a Isaki anakumba chitsime.


khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa chilumbiriro ndinachilumbirira kwa Abrahamu atate wako;


Taonani, Yehova anaima pamwamba pake, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isaki; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako;


akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu.


Ndipo Yakobo anatcha dzina la malo amenewo, Penuwele: chifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga.


Ndipo anamanga pamenepo guwa la nsembe, natcha pamenepo El-Elohe-Israele.


ndipo dziko limene ndinapatsa kwa Abrahamu ndi kwa Isaki ndidzalipatsa kwa iwe ndipo ndidzapatsa mbeu zako za pambuyo pako dzikoli.


Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, natcha pamenepo El Betele: pakuti kumeneko Mulungu anaonekera kwa iye muja anathawa pa nkhope ya mbale wake.


Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.


Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.


Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka chifukwa cha dziko, ndi mliri wa pa Israele unalekeka.


Ndipo ndi miyalayi anamanga guwa la nsembe m'dzina la Yehova, nazunguniza guwalo ndi mchera, ukulu wake ngati kulandira miyeso iwiri ya mbeu kuzinga guwalo.


chipanganocho anapangana ndi Abrahamu, ndi lumbiro lake ndi Isaki;


ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani, gawo la cholowa chako.


tapenyani, m'mene atibwezera, kudzatiinga m'cholowa chanu, chimene munatipatsa chikhale cholowa chathu.


Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m'dziko muno pamaso pa ana anu Israele, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha?


Nanyamuka Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake ansembe, ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, namanga guwa la nsembe la Mulungu wa Israele, kuperekapo nsembe zopsereza, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu.


Ndipo Mose anamanga guwa la nsembe, nalitcha dzina lake Yehova Nisi:


Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde paphiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele.


Kumbukirani Abrahamu, Isaki ndi Israele, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzitchula nokha, amene munanena nao, Ndidzachulukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale cholowa chao nthawi zonse.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kuchokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kuchokera m'dziko la Ejipito, kunka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo;


ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwike kwa iwo ndi dzina langa YEHOVA.


Ndipo ndinakhazikitsanso nao chipangano changa, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo ao, anali alendo m'mwemo.


Masiku omwewo nyumba ya Yuda idzayenderena ndi nyumba ya Israele, ndipo adzatuluka pamodzi kudziko la kumpoto kunka ku dziko limene ndinapatsa makolo anu kuti alowemo.


Dziko ligawikire iwowa monga mwa kuwerenga kwa maina, likhale cholowa chao.


Anthu adakwerawo kutuluka mu Ejipito, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo; popeza sananditsate Ine ndi mtima wonse;


ndipo sanampatse cholowa chake m'menemo, ngakhale popondapo phazi lake iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lake, ndi la mbeu yake yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.


Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yake.


Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Khristu.


Koma ife, abale, monga Isaki, tili ana a lonjezano.


Taonani, ndakupatsani dzikoli pamaso panu, lowani landirani dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuti ili ndidzawapatsa iwo ndi mbeu zao pambuyo pao.


kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ake, ndi kummamatira Iye, pakuti Iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.


Ndipo Yehova anati kwa iye, Si ili dziko ndinalumbirira Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzalipereka kwa mbeu zako. Ndinakuonetsa ili m'maso, koma sudzaolokako.


Ndipo kudzakhala, Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuti adzakupatsani ili; mizinda yaikulu ndi yokoma, imene simunaimange;


Simulowa kulandira dziko lao chifukwa cha chilungamo chanu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.


Iwo onse adamwalira m'chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.


Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.


Khala wamphamvu, nulimbike mtima, pakuti udzagawira anthu awa dzikoli likhale cholowa chao, ndilo limene ndinalumbirira makolo ao kuwapatsa.


Ndipo pamene anafikira mbali ya ku Yordani, ndilo la m'dziko la Kanani, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anamanga ku Yordani guwa la nsembe, guwa lalikulu maonekedwe ake.


Pomwepo Yoswa anamangira Yehova Mulungu wa Israele guwa la nsembe m'phiri la Ebala,


Pamenepo Gideoni anammangira Yehova guwa la nsembe pomwepo; nalitcha Yehova-ndiye-mtendere; likali mu Ofura wa Aabiyezere ndi pano pomwe.


Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yake inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israele; namangapo guwa la nsembe la Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa