2 Samueli 23:5 - Buku Lopatulika5 Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu; koma Iye anapangana ndi ine pangano losatha, lolongosoka mwa zonse ndi losungika; pakuti ichi ndi chipulumutso changa chonse, ndi kufuma kwanga konse, kodi sadzachimeretsa? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu; koma Iye anapangana ndi ine pangano losatha, lolongosoka mwa zonse ndi losungika; pakuti ichi ndi chipulumutso changa chonse, ndi kufuma kwanga konse, kodi sadzachimeretsa? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Motero Mulungu adzadalitsa zidzukulu zanga chifukwa Iye adachita nane chipangano chosatha, chipangano cholongosoka bwino ndi chosasinthika. Izi nzimene ndikulakalaka, ndiponso zimene zidzandipulumutsa. Ndi Mulungu amene adzachita zonsezi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 “Kodi banja langa silolungama pamaso pa Mulungu? Kodi Iye sanachite pangano losatha ndi ine, lokonzedwa ndi lotetezedwa mbali zonse? Kodi sadzakwaniritsa chipulumutso changa, ndi kundipatsa chokhumba changa chilichonse? Onani mutuwo |
Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m'njira zanga ndi kuchita chilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga pamenepo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga ndinammangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Israele.