Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 36:7 - Buku Lopatulika

7 Chifukwa chuma chao chinali chambiri chotero kuti sanakhoze kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoze kuwakwanira chifukwa cha ng'ombe zao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Chifukwa chuma chao chinali chambiri chotero kuti sanakhoze kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoza kuwakwanira chifukwa cha ng'ombe zao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Chimene adachokera ndi chakuti dziko limene ankakhalako iye pamodzi ndi Yakobe, silinkaŵakwanira aŵiriwo. Anali ndi zoŵeta zochuluka zedi, mwakuti sikudatheke kuti iwo akhale pa malo amodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Iwo anatero chifukwa dziko limene ankakhalamo silikanakwanira awiriwo. Iwowa anali ndi ziweto zochuluka motero kuti sakanatha kukhala pamodzi.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 36:7
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordani; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzake.


Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: chifukwa kuti chuma chao chinali chambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi.


Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wako.


akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu.


Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.


Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo tcherani khutu kulira kwanga; musakhale chete pa misozi yanga; Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu, wosakhazikika, monga makolo anga onse.


ndiponso musamange nyumba, musafese mbeu, musaoke mipesa, musakhale nayo; koma masiku anu onse mudzakhale m'mahema; kuti mukhale ndi moyo masiku ambiri m'dziko limene mukhalamo alendo.


Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa