Genesis 36:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo Esau anatenga akazi ake, ndi ana ake aamuna, ndi ana ake aakazi, ndi anthu onse a m'banja mwake, ndi ng'ombe zake, ndi zoweta zake, ndi zonse anali nazo anasonkhanitsa m'dziko la Kanani; ndipo ananka ku dziko losiyana patali ndi Yakobo mphwake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo Esau anatenga akazi ake, ndi ana ake amuna, ndi ana ake akazi, ndi anthu onse a m'banja mwake, ndi ng'ombe zake, ndi zoweta zake, ndi zonse anali nazo anasonkhanitsa m'dziko la Kanani; ndipo ananka ku dziko losiyana patali ndi Yakobo mphwake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Tsono Esau adatenga akazi ake, ana ake aamuna, ana ake aakazi ndi anthu onse a m'nyumba mwake, pamodzi ndi zoŵeta zake zonse, ndi katundu wake yense amene adampeza ku dziko la Kanani, ndipo adasiyana ndi mbale wake uja Yakobe, napita kukakhala ku dziko lina. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi ndi ena onse a pa banja pake. Anatenganso ziweto zake ndi ziweto zake zonse pamodzi ndi katundu wake yense amene anamupata ku Kanaani, ndipo anachoka ku dziko la Kanaani kupatukana ndi mʼbale wake Yakobo. Onani mutuwo |