Ndipo njoka inali yochenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu?
2 Akorinto 11:3 - Buku Lopatulika Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Njoka ndi kuchenjera kwake idanyenga Heva. Ndikuwopa kuti maganizo anu angaipitsidwe chimodzimodzi, ndipo mungaleke kudzipereka kwa Khristu ndi mtima wonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ndikuopa kuti monga Hava ananyengedwa ndi kuchenjera kwa njoka, mitima yanunso ingasocheretsedwe kuleka nʼkudzipereka moona mtima ndi modzipereka kwenikweni kwa Khristu. |
Ndipo njoka inali yochenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu?
Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.
chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.
Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.
kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima.
Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.
Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope.
Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.
koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.
Ndizizwa kuti msanga motere mulikupatuka kwa iye amene anakuitanani m'chisomo cha Khristu, kutsata Uthenga Wabwino wina;
ndicho chifukwa cha abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tili nao mwa Khristu Yesu, kuti akatichititse ukapolo.
Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene Yesu Khristu anaonetsedwa pamaso panu, wopachikidwa?
Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;
kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo;
Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzichepetsa mwini wake, ndi kugwadira kwa angelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula chabe ndi zolingalira za thupi lake, wosagwiritsa mutuwo,
Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;
Mwa ichi inenso, posalekereranso, ndinatuma kukazindikira chikhulupiriro chanu, kuti kapena woyesa akadakuyesani, ndipo chivuto chathu chikadakhala chopanda pake.
Monga ndinakudandaulira iwe utsalire mu Efeso, popita ine ku Masedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,
Pakuti alipo ambiri osamvera mau, olankhula zopanda pake, ndi onyenga, makamaka iwo akumdulidwe,
Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindule nazo.
Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osaweruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.
ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,
Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana Khristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Khristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi.
Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.
Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu.
Ndipo njokayo inalavula m'kamwa mwake, madzi ngati mtsinje, potsata mkazi, kuti mkaziyo akakokoleredwe nao.
Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.
Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi,