Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Yohane 2:18 - Buku Lopatulika

18 Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana Khristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Khristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana Khristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Khristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ananu, ino ndi nthaŵi yotsiriza. Mudamva kuti kukubwera Woukira Khristu, ndipo tsopano aoneka kale ambiri oukira Khristu. Zimenezi zikutizindikiritsa kuti ino ndi nthaŵi yotsirizadi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ana anga, ino ndi nthawi yotsiriza, ndipo monga munamva kale kuti anthu okana Khristu akubwera, ngakhale tsopano okana Khristu ambiri afika kale. Zimenezi zikutisonyeza kuti ino ndi nthawi yotsiriza.

Onani mutuwo Koperani




1 Yohane 2:18
24 Mawu Ofanana  

Ndipo aneneri onama ambiri adzauka, nadzasokeretsa anthu ambiri.


chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.


Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Khristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.


Ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Iye; nadzasocheretsa ambiri.


Yesu ananena nao, Ananu, muli nako kanthu kakudya kodi? Anamyankha Iye, Iai.


Ndipo chitani ichi, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chili pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupirira.


Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika.


koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am'mwamba omwe;


amene anazindikirikatu lisanakhazikike dziko lapansi, koma anaonetsedwa pa chitsiriziro cha nthawi,


amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.


Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;


Koma padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m'tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha chitayiko chakudza msanga.


ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,


Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu siali Khristu? Iye ndiye wokana Khristu, amene akana Atate ndi Mwana.


Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.


ndipo mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu suchokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzimu wa wokana Khristu umene mudamva kuti ukudza; ndipo ulimo m'dziko lapansi tsopano lomwe,


Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.


kuti ananena nanu, Pa nthawi yotsiriza padzakhala otonza, akuyenda monga mwa zilakolako zosapembedza za iwo okha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa