Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Timoteyo 1:3 - Buku Lopatulika

3 Monga ndinakudandaulira iwe utsalire mu Efeso, popita ine ku Masedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Monga ndinakudandaulira iwe utsalire m'Efeso, popita ine ku Masedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pamene ndinkanyamuka kupita ku Masedoniya, paja ndidaakupempha kuti ukhalire ku Efeso. Kuli anthu ena kumeneko amene akuphunzitsa zina zachilendo, ndiye ndikufuna kuti iweyo uŵaletse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Monga ndinakupempha pamene ndinkapita ku Makedoniya, khala ku Efeso komweko kuti uletse anthu ena kuphunzitsa ziphunzitso zonyenga,

Onani mutuwo Koperani




1 Timoteyo 1:3
24 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.


koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m'ngalawa.


Pakuti kunakondweretsa a ku Masedoniya ndi Akaya kuchereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.


Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.


Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikire, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandire, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simunalandire, mulolana naye bwino lomwe.


Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;


koma ndikhulupirira mwa Ambuye kuti ine ndekhanso ndidzadza msanga.


Lamulira izi, nuziphunzitse.


Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa m'mauwo a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata;


Ndipo izi ulamulire, kuti akhale opanda chilema.


Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.


Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;


Ngati munthu aphunzitsa zina, wosavomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chiphunzitsocho chili monga mwa chipembedzo:


(Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye tsiku lijalo); ndi muja ananditumikira m'zinthu zambiri mu Efeso, uzindikira iwe bwino.


Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.


Komatu ndili nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.


Komatu ndili nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebele, wodzitcha yekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasocheretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa