Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 11:2 - Buku Lopatulika

2 Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Nsanje imene ndikukuchitirani ndi yonga ya Mulungu. Pakuti ndidakupalitsani ubwenzi ndi mwamuna mmodzi yekha, ngati namwali wangwiro ndi woyera mtima, kuti mukhale akeake a Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Nsanje imene ndimakuchitirani ndi yofanana ndi ya Mulungu. Ndinakulonjezani mwamuna mmodzi yekha, mwamunayo ndiye Khristu, kuti ndidzakuperekeni inuyo kwa Iyeyo monga namwali wangwiro.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 11:2
19 Mawu Ofanana  

Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.


Kungakhale kutenga amasiye kapena osudzulidwa akhale akazi ao, asachite; koma atenge anamwali a mbeu ya nyumba ya Israele, kapena wamasiye ndiye wamasiye wa wansembe.


Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira.


Chotero, abale anga, inunso munayesedwa akufa ku chilamulo ndi thupi la Khristu; kuti mukakhale ake a wina, ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa, kuti ife timbalire Mulungu zipatso.


Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino.


podziwa kuti Iye amene anaukitsa Ambuye Yesu adzaukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatiikapo pamodzi ndi inu.


Ndiopera inu, kuti kapena ndadzivutitsa ndi inu chabe.


Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m'phamphu la mwa Khristu Yesu.


amene timlalikira ife, ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyense mu nzeru zonse, kuti tionetsere munthu aliyense wamphumphu mwa Khristu;


monga mudziwa kuti tinachitira yense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha,


Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoyamba kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa