2 Akorinto 1:12 - Buku Lopatulika12 Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbu mtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Chimene timanyadira nchakuti mtima wathu umatichitira umboni kuti ponseponse pamene tidapita, koma makamakanso pakati panu, mayendedwe athu anali oyera ndi opanda chinyengo. Zinali choncho osati chifukwa chotsata nzeru za anthu ai, koma chifukwa Mulungu adatikomera mtima. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Tsono chonyadira chathu nʼchakuti, chikumbumtima chathu chimatitsimikizira kuti timakhala bwino mʼdziko lapansi, makamaka pa ubale wathu ndi inu. Takhala moona mtima ndi oyera mtima. Sitinachite chomwechi mwa nzeru ya dziko lapansi koma monga mwa chisomo cha Mulungu. Onani mutuwo |