2 Akorinto 11:4 - Buku Lopatulika4 Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikire, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandire, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simunalandire, mulolana naye bwino lomwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikira, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandira, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simunalandira, mulolana naye bwino lomwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Wina amati akabwera kudzalalika Yesu wina wosiyana ndi amene tidamlalika ife, inu mumangomulekerera. Kapena mukalandira mzimu wina wosiyana ndi Mzimu Woyera amene mudamlandira kale, inu nkumaloladi. Mwinanso mukalandira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene mudalandira kale, inu nkumauvomeradi msangamsanga. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Pakuti ngati wina abwera kwa inu nalalikira Yesu wina wosiyana ndi Yesu amene tinamulalikira, kapena ngati mulandira mzimu wina wosiyana ndi Mzimu amene munalandira, kapena uthenga wabwino wina wosiyana ndi umene munawuvomereza, inuyo mumangolandira mosavuta. Onani mutuwo |