Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, navutidwa; ndipo anagawa anthu anali nao ndi nkhosa ndi zoweta, ndi ngamira, zikhale makamu awiri;
1 Samueli 30:6 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Davide adavutika koopsa, pakuti anthu ankakamba zoti amponye miyala, chifukwa cha chisoni chao pokumbukira ana ao aamuna ndi aakazi. Koma Davide adapeza mphamvu mwa Chauta, Mulungu wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Davide anavutika kwambiri mu mtima mwake chifukwa anthu amakamba zoti amuponye miyala popeza aliyense anali ndi chisoni pokumbukira ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anapeza mphamvu mwa Yehova Mulungu wake. |
Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, navutidwa; ndipo anagawa anthu anali nao ndi nkhosa ndi zoweta, ndi ngamira, zikhale makamu awiri;
Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ake kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga chimbalangondo chochilanda ana ake kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu.
Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wake ulikumuwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ichi.
Angakhale andipha koma ndidzamlindira; komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pake.
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva mu Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.
Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya, pa mkokomo wa matiti anu; mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.
Ndilanditseni, Mulungu wanga, m'dzanja la woipa, m'dzanja la munthu wosalungama ndi wachiwawa.
Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.
Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? Atsala pang'ono kundiponya miyala.
Chifukwa Inu mwakhala linga la aumphawi, linga la osowa m'kuvutidwa kwake, pobisalira chimphepo, mthunzi wa pa dzuwa, pamene kuomba kwa akuopsa kufanana ndi chimphepo chakuomba tchemba.
Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.
Ndipo anati, Ndinaitana Yehova m'nsautso wanga, ndipo anandiyankha ine; ndinafuula ndili m'mimba ya manda, ndipo munamva mau anga.
Koma khamu lonse lidati liwaponye miyala. Ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka m'chihema chokomanako kwa ana onse a Israele.
Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana mu Kumwambamwamba!
Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Khristu? Onse anati, Apachikidwe pamtanda.
Amene anakhulupirira nayembekeza zosayembekezeka, kuti iye akakhale kholo la mitundu yambiri ya anthu, monga mwa chonenedwachi, Mbeu yako idzakhala yotere.
ndipo poyang'anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeke chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m'chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu,
Koma ngati tisautsidwa, kuli chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva.
Pakutinso pakudza ife Masedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m'katimo mantha.
Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?
Koma ana a Dani anati kwa iye, Mau ako asamveke ndi ife, angakugwere anthu owawa mtima, nukataya moyo wako ndi wa iwo a m'nyumba mwako.
Koma anthu, ndiwo amuna a Israele, anadzilimbitsa nanikanso nkhondo kumene anandandalika tsiku loyambalo.
Ndipo Yonatani mwana wa Saulo ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, namlimbitsa dzanja lake mwa Mulungu.
Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita.