1 Samueli 28:15 - Buku Lopatulika15 Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Pamenepo Samuele adafunsa Saulo kuti, “Chifukwa chiyani wandivuta ponditulutsa kuti ndibwere kuno?” Saulo adayankha kuti, “Ndavutika kwambiri, pakuti Afilisti abwera kudzandithira nkhondo, ndipo Mulungu wandifulatira osandiyankhanso, ngakhale podzera mwa aneneri, kapena m'maloto. Nchifukwa chake ndakuitanani kuti mundiwuze zomwe ndiyenera kuchita.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Samueli anafunsa Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandivutitsa pondiyitana kuti ndibwere kuno?” Sauli anayankha kuti, “Ine ndavutika kwambiri mʼmaloto. Afilisti akumenyana nane, ndipo Mulungu wandifulatira. Iye sakundiyankhulanso, ngakhale kudzera mwa aneneri kapena maloto. Choncho ndakuyitanani kuti mundiwuze zoti ndichite.” Onani mutuwo |