Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 28:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo Samuele ananena naye, Ndipo undifunsiranji ine, popeza Yehova anakuchokera, nasandulika mdani wako?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo Samuele ananena naye, Ndipo undifunsiranji ine, popeza Yehova anakuchokera, nasandulika mdani wako?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Samuele adati, “Chifukwa chiyani ukufuna ine tsopano, chikhalirecho Chauta wakufulatira kale ndipo wasanduka mdani wako?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Samueli anati, “Nʼchifukwa chiyani ukundifunsa ine, pakuti tsopano Yehova wakufulatira ndipo wasanduka mdani wako?

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 28:16
10 Mawu Ofanana  

Nati iye, Akapanda kukuthandiza Yehova, ndikaona kuti kokuthandiza ine? Kudwale kodi, kapena popondera mphesa?


Wathifula uta wake ngati mdani, waima ndi dzanja lake lamanja ngati mmaliwongo; wapha onse okondweretsa maso; watsanulira ukali wake ngati moto pahema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.


Ambuye wasanduka mdani, wameza Israele; wameza zinyumba zake zonse, wapasula malinga ake; nachulukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi chibumo.


Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.


Ndipo momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.


Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda Inu akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake. Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai.


Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita.


Ndipo Yehova yekha wachita monga ananena pakamwa panga; ndipo Yehova wang'amba ufumuwo, kuuchotsa m'dzanja lako, ndi kuupatsa mnansi wako, ndiye Davide.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa