Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 14:10 - Buku Lopatulika

10 Koma khamu lonse lidati liwaponye miyala. Ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka m'chihema chokomanako kwa ana onse a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Koma khamu lonse lidati liwaponye miyala. Ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka m'chihema chokomanako kwa ana onse a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Koma mpingo wonse udaati uŵaponye miyala. Pomwepo ulemerero wa Chauta udaonekera Aisraele onse m'chihema chamsonkhano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Koma gulu lonse linayankhula zofuna kuwagenda miyala. Pamenepo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa Aisraeli onse ku tenti ya msonkhano.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 14:10
14 Mawu Ofanana  

Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele kuti iwo anatembenukira kuchipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.


ndi m'mawa mwake mudzaona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife chiyani, kuti mutidandaulira ife?


Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? Atsala pang'ono kundiponya miyala.


Pamenepo mtambo unaphimba chihema chokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisiyo.


Ndipo Mose ndi Aroni analowa ku chihema chokomanako, natuluka, nadalitsa anthu; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse.


Ndipo Kora anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana nao ku khomo la chihema chokomanako; ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka kwa khamu lonse.


Ndipo kunali, posonkhanidwa khamulo kutsutsana nao Mose ndi Aroni, kuti anacheukira chihema chokomanako; taonani, mtambo unachiphimba, ndi ulemerero wa Yehova unaoneka.


Ndipo Mose anaika ndodozo pamaso pa Yehova m'chihema cha mboni.


Ndipo Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa msonkhano kunka ku khomo la chihema chokomanako, nagwa nkhope zao pansi; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera iwo.


Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafune ai!


Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunze? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;


Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.


Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa