Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 23:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo Yonatani mwana wa Saulo ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, namlimbitsa dzanja lake mwa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo Yonatani mwana wa Saulo ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, namlimbitsa dzanja lake mwa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsono Yonatani, mwana wa Saulo, adanyamuka napita kwa Davide ku Horesi, ndipo adamlimbitsa mtima pomuuza kuti Mulungu adzamteteza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ndipo Yonatani mwana wa Sauli anapita kwa Davide ku Horesi ndipo anamulimbitsa mtima pomuwuza kuti Yehova ali naye.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 23:16
16 Mawu Ofanana  

Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma.


Koma ndikadakulimbikitsani ndi m'kamwa mwanga, ndi chitonthozo cha milomo yanga chikadatsitsa chisoni chanu.


Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.


Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima, ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu.


Popeza mwamvetsa chisoni ndi mabodza mtima wa wolungama, amene sindinamvetse chisoni Ine, ndi kumlimbitsa manja woipa, kuti asabwerere kuleka njira yake yoipa, ndi kusungidwa wamoyo;


koma ndinakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.


Ndipo anamuonekera Iye mngelo wa Kumwamba namlimbitsa Iye.


Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake.


Koma langiza Yoswa, numlimbitse mtima, ndi kumkhwimitsa, pakuti adzaoloka pamaso pa anthu awa, nadzawalandiritsa dziko ulionali likhale laolao.


Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m'chisomo cha mwa Khristu Yesu.


Ndipo Davide anaona kuti Saulo adatuluka kudzafuna moyo wake; Davide nakhala m'chipululu cha Zifi m'nkhalango ku Horesi.


Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa