Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yohane 8:59 - Buku Lopatulika

59 Pamenepo anatola miyala kuti amponye Iye; koma Yesu anabisala, natuluka mu Kachisi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

59 Pamenepo anatola miyala kuti amponye Iye; koma Yesu anabisala, natuluka m'Kachisi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

59 Pamenepo Ayuda aja adayamba kutola miyala kuti amlase. Koma Yesu adazemba natuluka m'Nyumba ya Mulunguyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

59 Pamenepo iwo anatola miyala kuti amugende, koma Yesu anabisala, nachoka mozemba mʼNyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 8:59
18 Mawu Ofanana  

Ndipo anachititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, aang'ono ndi aakulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo.


Ndi iye wakuchitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu; khamu lonse limponye miyala ndithu; mlendo ndi wobadwa m'dziko yemwe akachitira dzina la Yehova mwano, awaphe.


Ndipo Afarisi anatuluka, nakhala upo womchitira Iye mwa kumuononga.


Ndipo maso ao anatseguka, ndipo anamzindikira Iye; ndipo anawakanganukira Iye, nawachokera.


Chifukwa chake Yesu sanayendeyendenso poonekera mwa Ayuda, koma anachokapo kunka kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efuremu; nakhala komweko pamodzi ndi ophunzira ake.


Ophunzira ananena ndi Iye, Rabi, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi?


Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako. Izi Yesu analankhula, nachoka nawabisalira.


Ndipo Pilato anati kwa iwo, Mumtenge Iye inu, ndi kumweruza Iye monga mwa chilamulo chanu. Ayuda anati kwa iye, Tilibe ulamuliro wakupha munthu aliyense;


Koma wochiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani; pakuti Yesu anachoka kachetechete, popeza panali anthu aunyinji m'malo muja.


Ndipo popita, anaona munthu ali wosaona chibadwire.


Koma anafuula ndi mau aakulu, natseka m'makutu mwao, namgumukira iye ndi mtima umodzi;


Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa