Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


65 Mau a Mulungu Okhudza Nyumba Yake Yopatulika

65 Mau a Mulungu Okhudza Nyumba Yake Yopatulika

Kuyambira kalekale, Mulungu walamula anthu ake kumanga Nyumba Yake Yopatulika, komwe tingachite miyambo Yake Yopatulika. Chifukwa Ambuye amabwera ku Nyumba Yake Yopatulika ndi ulemerero Wake, tiyenera kulemekeza nthawi zonse tikapezeka kutchalitchi, kaya tikupembedza kapena tikumvetsera mawu a Mulungu.

Mose ndi ana a Israeli anamanga chihema chopatulika chomwe chinali ngati kachisi koyenda nako paulendo wawo wotuluka mu Igupto. Kachisi wodziwika kwambiri m’Chipangano Chakale ndi uja womangidwa mu Yerusalemu nthawi ya Solomoni (2 Mbiri 2–5).

Masiku ano, kachisi waukulu kwambiri komwe Mulungu akufuna kukhala ndi mtima wako. Konzekeretsa malo okongola mkati mwako komwe Mzimu Woyera angakhalemo mosangalala ndipo asafune kuchoka.




1 Akorinto 6:19-20

Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa? Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:16

Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 8:10-11

Ndipo kunachitika atatuluka ansembe m'malo opatulika, mtambo unadzaza nyumba ya Yehova. Ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 7:1-2

Atatha tsono Solomoni kupemphera, moto unatsika kumwamba, nunyeketsa nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza nyumbayi. Ndipo tsiku la makumi awiri ndi chitatu la mwezi wachisanu ndi chiwiri anawauza anthu apite ku mahema ao, akusekera ndi kukondwera m'mtima mwao chifukwa cha zokoma Yehova adawachitira Davide, ndi Solomoni, ndi Aisraele anthu ake. Momwemo Solomoni anatsiriza nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu; ndipo zilizonse zidalowa mumtima mwake mwa Solomoni kuzichita m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba yakeyake, anachita mosalakwitsa. Ndipo Yehova anaonekera kwa Solomoni usiku, nanena naye, Ndamva pemphero lako, ndadzisankhira malo ano akhale nyumba ya nsembe. Ndikatseka kumwamba kuti pasakhale mvula, kapena ndikalamulira dzombe lithe za padziko, kapena ndikatumiza mliri mwa anthu anga; ndipo anthu anga otchedwa dzina langa akadzichepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera mu Mwamba, ndi kukhululukira choipa chao, ndi kuchiritsa dziko lao. Tsopano maso anga adzakhala otsegukira, ndi makutu anga otchera, pemphero la m'malo ano. Pakuti ndasankha ndi kuipatula nyumba iyi, kuti dzina langa likhaleko chikhalire; inde maso anga ndi mtima wanga zidzakhala komweko kosalekeza. Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga monga umo anayendera Davide atate wako, nukachita monga mwa zonse ndakulamulira iwe, nukasunga malemba anga ndi maweruzo anga; pamenepo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wa ufumu wako, monga ndinapangana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wokhala mfumu mu Israele. Koma mukabwerera inu, ndi kusiya malemba anga, ndi malamulo anga, amene ndaika pamaso panu, ndi kumuka ndi kutumikira milungu ina ndi kuilambira; Ndipo ansembe sanakhoze kulowa m'nyumba ya Yehova, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 3:10-11

Ndipo pomanga maziko a Kachisi wa Yehova, amisiriwo anaimiritsa ansembe ovala zovala zao ndi mphalasa, ndi Alevi ana a Asafu ndi nsanje, kuti alemekeze Yehova, monga umo anaikiratu Davide mfumu ya Israele. Ndipo anathirirana mang'ombe, kulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi kuti, Pakuti ndiye wabwino, pakuti chifundo chake nchosalekeza pa Israele. Nafuula anthu onse ndi chimfuu chachikulu, pomlemekeza Yehova; popeza adamanga maziko a nyumba ya Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:10

Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:12-13

Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda; nanena kwa iwo, Chalembedwa, Nyumba yanga idzanenedwa nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 2:19-21

Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani Kachisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa. Ndipo Yesu yemwe ndi ophunzira ake anaitanidwa kuukwatiwo. Pamenepo Ayuda anati, Zaka makumi anai ndi zisanu ndi chimodzi analimkumanga Kachisiyu, kodi inu mudzamuutsa masiku atatu? Koma Iye analikunena za Kachisi wa thupi lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:17

Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:6

M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva mu Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 43:4-5

Ndipo ulemerero wa Yehova unalowa mu Kachisi kudzera njira ya chipata choloza kum'mawa. Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane kubwalo la m'kati; ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:4

Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 65:4

Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, akhale m'mabwalo anu. Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, za m'malo oyera a Kachisi wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:8

Ndipo andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:46-47

Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona; nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:16

Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 9:3

Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:42

Ndipo masiku onse, mu Kachisi ndi m'nyumba, sanaleke kuphunzitsa ndi kulalikira Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:22

Ndipo sindinaone Kachisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kachisi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:12

Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 11:4

Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:5

inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:21-22

mwa Iye chimango chonse cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale Kachisi wopatulika mwa Ambuye; chimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa Mzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 7:2

Ndipo ansembe sanakhoze kulowa m'nyumba ya Yehova, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:23

Ndipo m'mene Iye analowa mu Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 5:7

Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 26:8

Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu, ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:19-22

Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu, Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbumtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi? pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa chotchinga, ndicho thupi lake; ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu; tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 6:12-13

Kunena za nyumba ino ulikuimanga, ukamayenda iwe m'malemba anga, ndi kumachita maweruzo anga, ndi kumasunga malamulo anga onse kuyendamo, pamenepo Ine ndidzakhazikitsira iwe mau anga amene ndinauza Davide atate wako. Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israele osawasiya anthu anga a Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 8:27

Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:4

Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 7:4

Musakhulupirire mau onama, kuti, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova ndi awa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:12

Iye wakupambana, ndidzamyesa iye mzati wa mu Kachisi wa Mulungu wanga, ndipo kutuluka sadzatulukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika mu Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 6:40

Tsopano Mulungu wanga, maso anu akhale chipenyere, ndi makutu anu chimvere, pemphero lochitika pamalo pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 6:16

Ndipo ana a Israele, ansembe ndi Alevi, ndi ana otsala a ndende, anapereka nyumba iyi ya Mulungu mokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 37:26-28

Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha. Kachisi wanganso adzakhala nao, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga. Ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakupatula Israele, pokhala pakati pao malo anga opatulika kosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 7:48-49

Komatu Wamwambamwambayo sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena, Thambo la kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga, ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga. Mudzandimangira nyumba yotani, ati Ambuye, kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:11

Koma atafika Khristu, Mkulu wa ansembe wa zokoma zilinkudza, mwa chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:24

Pakuti Khristu sanalowe m'malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu mu Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:34-35

Pamenepo mtambo unaphimba chihema chokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisiyo. Ndipo Mose sanathe kulowa m'chihema chokomanako, popeza mtambo unakhalabe pamenepo; ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 7:5

Kauze mtumiki wanga Davide, kuti, Atero Yehova, Kodi iwe udzandimangira nyumba yakuti ndikhalemo Ine?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 22:19

Perekani tsono mtima ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu; ndipo nyamukani ndi kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti abwere nalo likasa la chipangano la Yehova, ndi zipangizo zopatulika za Mulungu, kunyumba imene idzamangidwira dzina la Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 7:15

Chifukwa chake ali kumpando wachifumu wa Mulungu; ndipo amtumikira Iye usana ndi usiku mu Kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawachitira mthunzi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 6:12-13

nunene naye, kuti, Atero Yehova wa makamu, ndi kuti, Taonani, munthu dzina lake ndilo Mphukira, ndipo adzaphuka m'malo mwake, nadzamanga Kachisi wa Yehova: inde adzamanga Kachisi wa Yehova; nadzasenza ulemererowo, nadzakhala ndi kulamulira pa mpando wachifumu wake; nadzakhala wansembe pampando wachifumu wake; ndi uphungu wa mtendere udzakhala pakati pa iwo awiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:6

Koma ndinena kwa inu, kuti wakuposa Kachisiyo ali pompano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 5:5

Ndipo taonani, ndikuti ndimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, monga Yehova anauza atate wanga Davide, ndi kuti, Mwana wako ndidzamuika pa mpando wako wachifumu m'malo mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumbayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 1:2-3

Atero Kirusi mfumu ya ku Persiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a padziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba mu Yerusalemu, ndiwo mu Yuda. Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, akwere kunka ku Yerusalemu, ndiwo mu Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israele; Iye ndiye Mulungu wokhala mu Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hagai 2:9

Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m'malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 4:23-24

Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m'choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 29:9

Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi, ndipo lipulula nkhalango; ndipo mu Kachisi mwake zonse zili m'mwemo zimati, Ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:33

pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 8:30

Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisraele, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 5:13-14

Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova; ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo; pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:12-13

Pamenepo mudzandiitana Ine, ndipo mudzanka ndi kupemphera kwa Ine, ndipo ndidzakumverani inu. Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 6:1-4

Chaka chimene mfumu Uziya anafa, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando wachifumu wautali, ndi wotukulidwa, ndi zovala zake zinadzala mu Kachisi. Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, nachiritsidwe. Pompo ndinati ine, Ambuye mpaka liti? Ndipo anayankha, Mpaka mizinda ikhala bwinja, yopanda wokhalamo, ndi nyumba zopanda munthu, ndi dziko likhala bwinja ndithu, ndipo Yehova wasunthira anthu kutali, ndi mabwinja adzachuluka pakati padziko. Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m'menemo, lidzadyedwanso; monga kachere, ndi monganso thundu, imene tsinde lake likhalabe ataigwetsa; chotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lake. Pamwamba pa Iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; awiri anaphimba nao nkhope yake, awiri naphimba nao mapazi ake, awiri nauluka nao. Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake. Ndipo maziko a ziundo anasunthika ndi mau amene anafuula, ndipo nyumba inadzazidwa ndi utsi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:1

Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 28:6

Ndipo anati kwa ine, Solomoni mwana wako ndiye adzandimangira nyumba yanga ndi mabwalo anga; pakuti ndamsankha akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala atate wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 11:1

Ndipo anandipatsa ine bango ngati ndodo, ndi kuti, Tanyamuka, nuyese Kachisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 2:4

amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:1

Ndipo Yesu anatuluka ku Kachisi; ndipo ophunzira ake anadza kudzamuonetsa chimangidwe cha Kachisiyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 56:7

naonso ndidzanka nao kuphiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m'nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zao zopsereza ndi nsembe zao zidzalandiridwa paguwa langa la nsembe; pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 3:3

ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samuele nagona mu Kachisi wa Yehova, m'mene munali likasa la Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 6:12

nunene naye, kuti, Atero Yehova wa makamu, ndi kuti, Taonani, munthu dzina lake ndilo Mphukira, ndipo adzaphuka m'malo mwake, nadzamanga Kachisi wa Yehova:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 8:10

Ndipo kunachitika atatuluka ansembe m'malo opatulika, mtambo unadzaza nyumba ya Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 6:1

Ndipo kunachitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, chaka chachinai chakukhala Solomoni mfumu ya Israele, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi wachiwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Wamphamvuzonse! Ndimakulambirani, ndikuvomereza ukulu wanu ndi ulemerero wanu, ndaona kukoma mtima kwanu pa moyo wanga ndi chifundo chanu chachikulu. Atate, ndikufuna kukhala m'nyumba mwanu ndikhale ndi abale anga pamodzi mwamtendere, chifukwa kumeneko mumatumiza madalitso anu ndi moyo wosatha. Zikomo chifukwa kumeneko ndi komwe ndimakumana ndi ena komwe ndingalimangire ndikupeza chilakolako chotumikira ufumu wanu, komwe ndingakwaniritse cholinga chanu ndi masomphenya a moyo. Ndikupemphani kuti tsiku lililonse m'mtima mwanga mukhale chikhumbo ndi chilakolako chosonkhana ndikukupatsani nthawi zonse ulemerero wanga wabwino kwambiri. Ndikukuthokozani chifukwa cha nyumba yanu chifukwa kumeneko ndi komwe anthu aamuna, akazi ndi anthu amitundu yonse amapempherera. Mawu anu amati: "Ndidzawatenga kupita ku phiri langa lopatulika, ndipo ndidzawasangalatsa m'nyumba yanga yopempherera; nsembe zawo zopsereza ndi nsembe zawo zidzalandiridwa pa guwa langa la nsembe, chifukwa nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopempherera anthu a mitundu yonse." Zikomo, Ambuye, chifukwa m'nyumba mwanu muli mphamvu yauzimu ndi chitetezo, chifukwa tsiku loipa mudzandibisira m'chihema chanu. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa