Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Hagai 2:9 - Buku Lopatulika

9 Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m'malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m'malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Choncho ulemerero wa Nyumba yachiŵiriyi udzaposa ulemerero wa Nyumba yoyamba ija. Ndipo ndidzakhazikitsa ufulu ndi mtendere pa malo ano. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 ‘Ulemerero wa nyumba iyi udzaposa ulemerero wa nyumba yoyamba ija,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ndipo pamalo pano ndidzakhazikitsapo mtendere,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

Onani mutuwo Koperani




Hagai 2:9
20 Mawu Ofanana  

Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebayoti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa paguwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.


Pakuti atero Yehova, Taonani ndidzamfikitsira mtendere ngati mtsinje, ndi ulemerero wa amitundu ngati mtsinje wosefukira. Inu mudzayamwa, ndi kunyamulidwa pambali, ndi kululuzidwa pa maondo.


Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane kubwalo la m'kati; ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.


Ndipo ameneyo adzakhala mtendere; pamene a ku Asiriya adzalowa m'dziko lathu, ndi pamene adzaponda m'zinyumba zathu, tidzawaukitsira abusa asanu ndi awiri, ndi akalonga asanu ndi atatu.


Kwerani kudziko la mapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa, ati Yehova.


Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi mu ulemerero wake woyamba? Ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m'maso mwanu ngati chabe?


Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pake, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwake.


Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.


Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse)


Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.


Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa