Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 21:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayamba kutulutsa onse amene ankachita malonda m'menemo. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama, ndiponso mipando ya ogulitsa nkhunda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Yesu analowa mʼdera lina la Nyumba ya Mulungu ndipo anatulutsa kunja anthu onse amene ankachita malonda. Anagubuduza matebulo a osinthira ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 21:12
18 Mawu Ofanana  

Ichi achipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri,) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo chopereka cha Yehova.


Ndipo chopereka chake cha kwa Yehova chikakhala nsembe yopsereza ya mbalame, azibwera nacho chopereka chake chikhale cha njiwa, kapena cha maunda.


Ndipo atakwanira masiku a kumyeretsa kwake pa mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, adze naye mwanawankhosa wa chaka chimodzi ikhale nsembe yopsereza, ndi bunda, kapena njiwa zikhale nsembe yauchimo, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe;


Ichi ndi chilamulo cha kwa iye wakubala, kapena mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziwiri kapena maunda awiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yauchimo; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala woyera.


ndi njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, monga akhoza kufikana; limodzi likhale la nsembe yauchimo, ndi linzake la nsembe yopsereza.


Ndipo iye apereke imodzi ya njiwazo, kapena limodzi la maunda, monga akhoza kufikana nazo,


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike pamaso pa Yehova pa khomo la chihema chokomanako, nazipereke kwa wansembe;


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike nazo kwa wansembe ku khomo la chihema chokomanako.


Koma chuma chake chikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wochimwayo azidza nacho chopereka chake limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yauchimo; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo lubani ai; pakuti ndicho nsembe yauchimo.


Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yake yopalamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yauchimo, ndi ina ya nsembe yopsereza.


Ndipo Iye analowa mu Yerusalemu, mu Kachisi; ndipo m'mene anaunguza zinthu zonse, popeza ndi madzulo, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.


ndi kukapereka nsembe monga mwanenedwa m'chilamulo cha Ambuye, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri.


Ndipo Paska wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa