Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 5:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo taonani, ndikuti ndimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, monga Yehova anauza atate wanga Davide, ndi kuti, Mwana wako ndidzamuika pa mpando wako wachifumu m'malo mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumbayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo taonani, ndikuti ndimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, monga Yehova anauza atate wanga Davide, ndi kuti, Mwana wako ndidzamuika pa mpando wako wachifumu m'malo mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumbayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Choncho ndikufuna kumangira nyumba Chauta Mulungu wanga, monga momwe Iye adaauzira bambo wanga Davide kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamukhazike pa mpando wako waufumu m'malo mwako, ndiye amene adzandimangire nyumba.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Choncho ine ndikufuna kumangira nyumba Yehova Mulungu wanga, monga momwe Iye anawuzira abambo anga Davide kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamukhazike pa mpando waufumu mʼmalo mwako ndiye adzandimangire Nyumba.’

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 5:5
15 Mawu Ofanana  

Koma usamange ndiwe nyumbayo, koma mwana wako adzatuluka m'chuuno mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumba.


Musamvere Hezekiya; pakuti itero mfumu ya Asiriya, Mupangane nane zamtendere, nimutulukire kwa ine, ndi kumadya yense ku mpesa wake, ndi yense ku mkuyu wake, ndi kumwa yense madzi a m'chitsime chake;


Iye adzandimangira nyumba; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wake kosatha.


iyeyu adzamangira dzina langa nyumba; iye adzakhala mwana wanga, ndi Ine ndidzakhala Atate wake; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wa ufumu wake pa Israele, kosalekeza.


Chenjera tsono, pakuti Yehova anakusankha iwe umange nyumba ya malo opatulika; limbika, nuchite.


Ndipo anati kwa ine, Solomoni mwana wako ndiye adzandimangira nyumba yanga ndi mabwalo anga; pakuti ndamsankha akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala atate wake.


M'mwemo muchite malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; ndipo mudzakhala m'dzikomo okhazikika.


Dziko lidzaperekanso zipatso zake, ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kukhalamo okhazikika.


Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.


Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wake patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu.


Ndipo Israele akhala mokhazikika pa yekha; kasupe wa Yakobo; akhala m'dziko la tirigu ndi vinyo; inde thambo lake likukha mame.


Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa