Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ahebri 9:24 - Buku Lopatulika

24 Pakuti Khristu sanalowe m'malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu mu Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Pakuti Khristu sanalowa m'malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu m'Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Paja Khristu sadaloŵe m'malo opatulika omangidwa ndi anthu, malo ongofanizira malo enieni opatulika a Kumwamba. Iye adapita Kumwamba kwenikweniko, kuti tsopano aziwonekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 9:24
32 Mawu Ofanana  

Munakwera kunka kumwamba, munapita nao undende kuuyesa ndende; munalandira zaufulu mwa anthu, ngakhale mwa opikisana nanu, kuti Yehova Mulungu akakhale nao.


Ndipo uiike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israele; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ake awiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova.


Ndipo Aroni azinyamula maina a ana a Israele pa chapachifuwa cha chiweruzo pamtima pake, pakulowa iye m'malo opatulika, akhale chikumbutso pankhope pa Yehova kosalekeza.


Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima padzanja lake lamanja, atsutsana naye.


Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.


Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kachisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja.


Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala padzanja lamanja la Mulungu.


Ndipo kunali, pakuwadalitsa Iye analekana nao, natengedwa kunka Kumwamba.


Ndinatuluka mwa Atate, ndipo ndadza kudziko lapansi: ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate.


Nanga bwanji ngati mukaona Mwana wa Munthu alikukwera kumene anali kale lomwe?


amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m'kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire.


Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? Mulungu ndiye amene awayesa olungama;


Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, mu Mwamba.


Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.


ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala padzanja lamanja la Ukulu mu Mwamba,


Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.


Popeza tsono tili naye Mkulu wa ansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu.


m'mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa chihema choona, chimene Ambuye anachimanga, si munthu ai.


amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri.


Ndipo chingakhale chipangano choyambachi chinali nazo zoikika za kulambira, ndi malo opatulika a padziko lapansi.


Pomwepo padafunika kuti zifaniziro za zinthu za mu Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam'mwamba zenizeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi.


ndicho chiphiphiritso cha kunthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za chikumbumtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.


amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.


Ndipo anadza mngelo wina, naima paguwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolide; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse paguwa la nsembe lagolide, lokhala kumpando wachifumu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa