Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 9:11 - Buku Lopatulika

11 Koma atafika Khristu, Mkulu wa ansembe wa zokoma zilinkudza, mwa chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Koma atafika Khristu, Mkulu wa ansembe wa zokoma zilinkudza mwa, chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Koma Khristu wafika, ndipo ndiye Mkulu wa ansembe onse wa zokoma zimene zilikudza tsopano. Chihema chimene Iye amatumikiramo nchachikulu ndiponso changwiro kopambana. Nchosapangidwa ndi anthu, ndiye kuti si chapansipano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma Khristu atafika monga Mkulu wa ansembe wa zinthu zokoma zimene zilipo tsopano, Iye analowa mʼChihema chachikulu ndiponso changwiro chimene sichinamangidwe ndi munthu, ndiye kuti sichili pansi pano.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 9:11
30 Mawu Ofanana  

Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.


Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza; m'buku mwalembedwa za Ine,


Ndipo Mombolo adzafika ku Ziyoni, ndi kwa iwo amene atembenuka kusiya kulakwa mwa Yakobo, ati Yehova.


Ndipo ndidzawayeretsa kuchotsa mphulupulu yao, imene anandichimwira Ine; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu zao zimene anandichimwira, nandilakwira Ine.


Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.


nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina?


Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wamng'onong'ono mwa akulu a Yudeya. Pakuti Wotsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisraele.


Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kachisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja.


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Mkazi ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti Mesiya adza (wotchedwa Khristu): akadzadza Iyeyu, adzatiuza zonse.


Komatu Wamwambamwambayo sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena,


popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha.


Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, mu Mwamba.


amenenso munadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m'mavulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Khristu;


Pakuti chilamulo, pokhala nao mthunzi wa zokoma zilinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo, sichikhozatu, ndi nsembe zomwezi chaka ndi chaka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.


Ndipo ichi, chakuti kamodzinso, chilozera kusuntha kwake kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zikhale.


Pakuti pano tilibe mzinda wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo.


Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.


Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chivomerezo chathu, Yesu;


Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.


Pakuti Melkizedeki uyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa,


Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.


Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa