Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


101 Mauthenga a M'Baibulo Okhudza Ubatizo

101 Mauthenga a M'Baibulo Okhudza Ubatizo

Ubatizo ndi mwambo woyamba wa Uthenga Wabwino. Yesu Khristu analamulira atumwi ake kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani mitundu yonse ya anthu, muwabatize m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera, ndipo muziwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani; ndipo onani, Ine ndili pamodzi nanu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ino.” (Mateyu 28:19-20). Masiku ano, monga m’nthawi ya Yesu, pali mfundo ndi miyambo ya Uthenga Wabwino yomwe tiyenera kuphunzira ndi kutsatira.

Mfundo ya Uthenga Wabwino ndi chikhulupiriro kapena chiphunzitso choona; mwambo ndi mwambo kapena lamulo. Mfundo ziwiri zoyambirira za Uthenga Wabwino ndi chikhulupiriro mwa Ambuye Yesu Khristu ndi kulapa. Ndikukhulupirira kuti ngati tiphunzira ndikutsatira mfundo izi, tidzadalitsidwa kwambiri.




Machitidwe a Atumwi 2:38

Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:16

Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:27

Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:5

Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:3

Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:4

Yohane anadza nabatiza m'chipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku chikhululukiro cha machimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19

Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:26-27

Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19-20

Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 3:11

Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:21

chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:15

kuti yense wakukhulupirira akhale nao moyo wosatha mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 22:16

Ndipo tsopano uchedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane pa dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:5

Ndipo anatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordani, powulula machimo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:12

popeza munaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzi ndi Iye m'chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa Iye kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:47

Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:13

Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:3-4

Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yake? Chifukwa chake tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:47-48

Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife? Ndipo analamulira iwo abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Pamenepo anampempha iye atsotse masiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 3:16-17

Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 3:21-22

Pamene anthu onse anabatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Iye anali kupemphera, ndipo kuthambo kunatseguka, ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lake ngati nkhunda, nadza pa Iye; ndipo munatuluka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:2

Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:36-38

Ndipo monga anapita panjira pao, anadza kumadzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe? Ndipo anamuuza kuti aimitse galeta; ndipo anatsikira onse awiri kumadzi, Filipo ndi mdindoyo; ndipo anambatiza iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:5

Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:5

zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:4

Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:17

Pakuti Khristu sananditume ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Khristu ungayesedwe wopanda pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:5

Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m'chifanizidwe cha imfa yake, koteronso tidzakhala m'chifanizidwe cha kuuka kwake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:30-33

nawatulutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke? Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako. Ndipo anamuuza iye mau a Ambuye, pamodzi ndi onse a pabanja pake. Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 18:8

Ndipo Krispo, mkulu wa sunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupirira, nabatizidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:1

Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala padzanja lamanja la Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:50

Koma ndili ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:14

Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:44-48

Petro ali chilankhulire, Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo. Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha, Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife? Ndipo analamulira iwo abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Pamenepo anampempha iye atsotse masiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:41

Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:10

Pakuti pakufa Iye, atafa ku uchimo kamodzi; ndipo pakukhala Iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 3:13-15

Pamenepo Yesu anachokera ku Galileya nadza ku Yordani kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:6-8

Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi. Pakuti pali atatu akuchita umboni, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 11:16

Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 116:13

Ndidzanyamula chikho cha chipulumutso, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31-32

Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani? Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:47

nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:2

nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m'nyanja,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:1-2

Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe cha Khristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu, pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe. Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga kuchiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro; kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima. Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kumlumbira, analumbira pa Iye yekha, nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kuchulukitsa ndidzakuchulukitsa iwe. Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo. Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'chitsutsano chao chilichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza. Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mochulukira kwa olowa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analowa pakati ndi lumbiro; kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu; chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba; a chiphunzitso cha ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:9

ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m'lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:16

Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:40-41

Ndipo ndi mau ena ambiri anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota. Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:29

Ngati si kutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa saukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha iwo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:37-38

mauwo muwadziwa inu, adadzawo ku Yudeya lonse, akuyamba ku Galileya, ndi ubatizo umene Yohane anaulalikira; za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:18-20

Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi. Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:17

ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:12-14

ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao cholowa cha oyera mtima m'kuunika; amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake; amene tili nao maomboledwe mwa Iye, m'kukhululukidwa kwa zochimwa zathu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:12

Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:18

Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:16

Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:15-16

Ndipo ananena nao, Mukani kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse. Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:38-39

Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:47

ndi kuti kulalikidwe m'dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:1

Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:20

Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:19

Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:9

Pakuti chitsime cha moyo chili ndi Inu, M'kuunika kwanu tidzaona kuunika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:22

tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:10-12

ndipo muli odzazidwa mwa Iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro; amenenso munadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m'mavulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Khristu; popeza munaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzi ndi Iye m'chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa Iye kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:27

Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:13

pakuti, aliyense amene adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:46-47

Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha, Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:24

Koma iwo a Khristu Yesu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:7

koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:7

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:5-6

Pamene anamva ichi, anabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:11

Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:17

Pakuti m'menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:20

ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:9

Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, siali wake wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:15

Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:50

Chitonthozo changa m'kuzunzika kwanga ndi ichi; pakuti mau anu anandipatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:25

Ngati tili ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:23

inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:36-38

Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika. Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale? Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:12-14

Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake: ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo. Pakuti uchimo sudzachita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a chisomo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:14

ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:106

Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:19

Ndipo Iye ananena nao, Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:13-14

Ndipo inu, pokhala akufa m'zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m'mene adatikhululukira ife zolakwa zonse; adatha kutifafanizira cha pa ifecho cholembedwa m'zoikikazo, chimene chinali chotsutsana nafe: ndipo anachichotsera pakatipo, ndi kuchikhomera ichi pamtanda;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:12

Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Khristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:15

Pakuti inu simunalandire mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:15

Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:5

inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:27

Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira; mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:8-9

Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:41-42

Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu. Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:22

ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:3

Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:44

Petro ali chilankhulire, Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:7

Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye, ndinu Alfa ndi Omega! Atate, Mlengi wa thambo ndi dziko lapansi, ndinu woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi chimaliziro. Mulungu wokondedwa, munatiuza m'mawu anu kuti aliyense wokhulera mwa Mwana wanu Yesu ndi uthenga wanu abatizidwe. Chifukwa chake lero ndikupemphani kuti muvumbulutsire anthu anu osankhidwa kufunika ndi madalitso auzimu omwe amabwera chifukwa cha kubatizidwa. Yesu, ndinu chitsanzo chachikulu cha kumvera pobatizidwa mu mtsinje wa Yorodani. Ndi kumvera kwanu, titithandizeni kusintha ndi kukonzanso kudzera mwa Mzimu Woyera wanu m'batizo la madzi ndi malilime. Tsiku limenelo, munatipanga ana a Mulungu ndi olowa ufumu wanu. Tsiku limenelo, munatilandira monga mamembala a Mpingo kuti tikatenge uthenga wa chipulumutso ndi chiwombolo padziko lonse lapansi, kwa cholengedwa chilichonse. Mawu anu amati: “Nanga tsopano uchedwanji? Nyamuka, ubatizidwe, nutsitsidwe machimo ako, ndipo udzatchula dzina lake.” Ndipereka mitima ndi zilakolako za ana anu kwa Mzimu wanu wabwino, awapatse chikhulupiriro ndi chilakolako chochita malamulo anu m'miyoyo yawo, kuti tiyende m'chikondi wina ndi mnzake monga momwe mawu anu amanenera. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa