Ndikuganiza kuti dalitso la Mulungu ndi chuma ndi katundu basi, ndalakwitsa kwambiri. Zimenezi zikutanthauza kuti anthu osauka sadalitsidwa ndi Mulungu, kapena kuti Mulungu sawakonda. Sizoona kuganiza kuti Mulungu amalanga ena ndi umphawi, pomwe ena amawadalitsa ndi chuma.
Mawu a Mulungu amatipatsa zitsanzo za anthu okhulupirika ndi omvera kwa Iye, koma anali osauka. Nthawi zina timaona kugwirizana pakati pa dalitso ndi chuma, koma zoona zake n’zakuti Mulungu amatidalitsa m’njira zambiri, ngakhale m’mavuto ndi zovuta.
Tiyenera kukhala oyamikira nthawi zonse, chifukwa Mulungu amaona mtima wathu. Ambiri, akakula m’chuma kapena akapambana, amatamanda Mulungu ndi kumuthokoza panthawiyo, koma chimwemwe chathu ndi ubwino wathu ziyenera kuchokera kwa Mulungu osati pa ndalama.
Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yakoyako. Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.
Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamira ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.
Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi; ndi osowa ndalama idzani inu mugule mudye; inde idzani, mugule vinyo ndi mkaka opanda ndalama ndi opanda mtengo wake.
Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona.
Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!
Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo analemera kwakulukulu; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng'ombe, ndi siliva ndi golide, ndi akapolo ndi adzakazi, ndi ngamira ndi abulu.
Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wa mwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.
Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.
ndipo munganene m'mtima mwanu, Mphamvu yanga ndi mkono wanga wolimba zinandifunira chuma ichi. Koma mukumbukire Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera chuma; kuti akhazikitse chipangano chake chimene analumbirira makolo anu, monga chikhala lero lino.
Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.
Popeza simunatumikire Yehova Mulungu wanu ndi chimwemwe ndi mokondwera mtima, chifukwa cha kuchuluka zinthu zonse; chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.
Ndiponso zimene sunazipemphe adakupatsa, ndipo chuma ndi ulemu, kuti pakati pa mafumu sipadzakhala ina yolingana ndi iwe masiku ako onse.
Ndipo mfumu inachulukitsa siliva ngati miyala mu Yerusalemu, ndi mitengo yamikungudza anailinganiza ndi mikuyu ya m'madambo.
Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.
Yehova Mulungu wathu, zounjikika izi zonse tazikonzeratu kukumangirani Inu nyumba ya dzina lanu loyera zifuma ku dzanja lanu, zonsezi ndi zanu.
Ndipo Mulungu anati kwa Solomoni, Popeza chinali mumtima mwako ichi, osapempha chuma, akatundu, kapena ulemu, kapena moyo wa iwo akudana nawe, osapemphanso masiku ambiri; koma wadzipemphera nzeru ndi chidziwitso, kuti uweruze anthu anga amene ndakuika ukhale mfumu yao, nzeru ndi chidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso chuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhale nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.
Momwemo mfumu Solomoni inaposa mafumu onse a padziko lapansi, kunena za chuma ndi nzeru.
Ndipo chuma ndi ulemu zinachulukira Hezekiya, nadzimangira iye zosungiramo siliva, ndi golide, ndi timiyala ta mtengo wake, ndi zonunkhira, ndi zikopa, ndi zipangizo zokoma zilizonse; ndi nyumba zosungiramo zipatso za tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zipinda za nyama iliyonse, ndi makola a zoweta. Nadzimangiranso mizinda, nadzionera nkhosa ndi ng'ombe zochuluka; pakuti Mulungu adampatsa chuma chambirimbiri.
Panali munthu m'dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa. Kodi simunamtchinge iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m'dziko. Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu. Nati Yehova kwa Satana, Taona, zonse ali nazo zikhale m'dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako. Natuluka Satana pamaso pa Yehova. Tsono panali tsiku loti ana ake aamuna ndi aakazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkulu wao; nafika mthenga kwa Yobu, nati, Ng'ombe zinalikulima, ndi abulu aakazi analikudya pambali pao; koma anazigwera Aseba, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani. Akali chilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Wagwa moto wa Mulungu wochokera kumwamba, wapsereza nkhosa ndi anyamata, nuzinyeketsa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani. Akali chilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Ababiloni anadzigawa magulu atatu, nazigwera ngamira, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani. Akali chilankhulire, anadza winanso, nati, Ana anu aamuna ndi aakazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkulu wao; ndipo taonani, inadza mphepo yaikulu yochokera kuchipululu, niomba pangodya zonse zinai za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani. Ndipo anabala ana aamuna asanu ndi awiri, ndi ana aakazi atatu. Pamenepo Yobu ananyamuka, nang'amba malaya ake, nameta mutu wake, nagwa pansi, nalambira, nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova. Mwa ichi chonse Yobu sanachimwe, kapena kunenera Mulungu cholakwa. Zoweta zakenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi ngamira zikwi zitatu, ndi ng'ombe zamagoli mazana asanu, ndi abulu aakazi mazana asanu, antchito ake omwe ndi ambiri; chotero munthuyu anaposa anthu onse a kum'mawa.
Ndipo Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu, pamene anapempherera mabwenzi ake; Yehova nachulukitsa zake zonse za Yobu mpaka kuziwirikiza.
Iwo akutama kulemera kwao; nadzitamandira pa kuchuluka kwa chuma chao; kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kumperekera dipo kwa Mulungu.
Usaope polemezedwa munthu, pochuluka ulemu wa nyumba yake; pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kalikonse; ulemu wake sutsika naye kumtsata m'mbuyo.
Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyese Mulungu mphamvu yake; amene anatama kuchuluka kwa chuma chake, nadzilimbitsa m'kuipsa kwake.
Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.
M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire.
Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mzinda Yehova, mlonda adikira chabe. Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.
Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golide woyengeka.
Chuma cholandiridwa mokangaza chidzachepa; koma wokundika ndi dzanja adzaona zochuluka.
Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri; kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golide. Ukainga wonyoza, makangano adzatuluka; makani ndi manyazi adzalekeka. Wokonda kuyera mtima, mfumu idzakhala bwenzi lake chifukwa cha chisomo cha milomo yake. Maso a Yehova atchinjiriza wodziwa; koma agwetsa mau a munthu wa ziwembu. Waulesi ati, Pali mkango panjapo, ndidzaphedwa pamakwalalapo. M'kamwa mwa mkazi wachiwerewere muli dzenje lakuya; yemwe Yehova amkwiyira adzagwamo. Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali. Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake, ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka. Tchera makutu ako, numvere mau a anzeru, nulozetse mtima wako kukadziwa zanga. Pakuti mauwo akondweretsa ngati uwasunga m'kati mwako, ngati akhazikika pamodzi pa milomo yako. Ndakudziwitsa amenewo lero, ngakhale iwedi, kuti ukhulupirire Yehova. Wolemera ndi wosauka akumana, wolenga onsewo ndiye Yehova.
Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.
Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lake ndi kukondwera ndi ntchito zake; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu.
munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma ndi ulemu, mtima wake susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ichi ndi chabe ndi nthenda yoipa.
Dziko lao ladzala siliva ndi golide, ngakhale chuma chao nchosawerengeka; dziko lao lidzalanso akavalo, ngakhale magaleta ao ngosawerengeka.
Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m'nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wake adzacha bwino ndi kuchuluka; tsiku limenelo ng'ombe zako zidzadya m'madambo aakulu.
Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, chuma cha amitundu chidzafika kwa iwe.
Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake;
Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikire, momwemo iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ake chidzamsiya iye, ndipo pa chitsirizo adzakhala wopusa.
Adzataya siliva wao kumakwalala, nadzayesa golide wao chinthu chodetsedwa; siliva wao ndi golide wao sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova, sadzakwaniritsa moyo wao, kapena kudzaza matumbo ao; pakuti izi ndi chokhumudwitsa cha mphulupulu zao.
mwa nzeru zako ndi luntha lako wadzionerera chuma, wadzionereranso golide ndi siliva mwa chuma chako; mwa nzeru zako zazikulu ndi kugulana malonda kwako wachulukitsa chuma chako, ndi mtima wako wadzikuza chifukwa cha chuma chako;
Ndipo Efuremu anati, Zedi ndasanduka wolemera, ndadzionera chuma m'ntchito zonse ndinazigwira; sadzapeza mwa ine mphulupulu yokhala tchimo.
Funkhani siliva, funkhani golide; pakuti palibe kutha kwake kwa zosungikazo, kwa chuma cha zipangizo zofunika zilizonse.
Ndipo Tiro adzadzimangira polimbikirapo, nadzakundika siliva ngati fumbi, ndi golide woyenga ngati thope la kubwalo.
Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.
Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. koma mudzikundikire nokha chuma mu Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.
Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.
Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso.
Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?
Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate. Koma mnyamatayo m'mene anamva chonenacho, anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri.
Ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, Indetu ndinena kwa inu, kuti munthu mwini chuma adzalowa movutika mu Ufumu wa Kumwamba. Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamira ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.
Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake. Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye. Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu. Chimodzimodzi uyo wa awiriwo, anapindulapo ena awiri. Koma uyo amene analandira imodziyo anamuka, nakumba pansi, naibisa talente ya mbuye wake. Ndipo itapita nthawi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nao pamodzi. Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera. Ndipo uyo amene adalandira matalente asanu anadza, ali nawo matalente ena asanu, nanena, Mbuye, munandipatsa matalente asanu, onani ndapindulapo matalente ena asanu. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. Ndipo wa matalente awiriwo anadzanso, nati, Mbuye, munandipatsa ine matalente awiri; onani, ndapindulapo matalente ena awiri. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. Ndipo uyonso amene analandira talente imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafese, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaze; ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi talente yanu: onani, siyi talente yanuyo. Koma mbuye wake anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafese, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaze; chifukwa chake ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lake. Chifukwa chake chotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi. Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho. Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengerenso mafuta; Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda chipatso.
Ndipo Yesu anamyang'ana, namkonda, nati kwa iye, Chinthu chimodzi chikusowa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo chuma udzakhala nacho m'mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine. Koma nkhope yake inagwa pa mau awa, ndipo anachoka iye wachisoni; pakuti anali mwini chuma chambiri.
Ndipo Yesu anaunguzaunguza, nanena ndi ophunzira ake, Okhala nacho chuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu ndi kuvuta nanga! Ndipo ophunzirawo anazizwa ndithu ndi mau ake. Koma Yesu anayankhanso nanena nao, Ananu, nkovuta ndithu kwa iwo akutama chuma kulowa mu Ufumu wa Mulungu! Nkwa pafupi kuti ngamira ipyole diso la singano kuposa kuti mwini chuma alowe mu Ufumu wa Mulungu.
Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.
Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo. Ndipo Iye ananena nao fanizo, kuti, Munda wake wa munthu mwini chuma unapatsa bwino. Ndipo anaganizaganiza mwa yekha nanena, Ndidzatani ine, popeza ndilibe mosungiramo zipatso zanga? Ndipo anati Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi chuma changa. Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere. Koma kulibe kanthu kovundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika. Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani? Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.
Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha mu Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga. Pakuti kumene kuli chuma chanu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.
Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.
Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa chinthu chimodzi: gulitsa zilizonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma chenicheni mu Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine. Koma pakumva izi anagwidwa nacho chisoni chambiri; pakuti anali mwini chuma chambiri.
Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! Nkuvutika nanga kwa anthu eni chuma kulowa Ufumu wa Mulungu! Pakuti nkwapafupi kwa ngamira ipyole diso la singano koma kwa munthu mwini chuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali.
Yohane anayankha nati, Munthu sangathe kulandira kanthu, ngati sikapatsidwa kwa iye kuchokera Kumwamba.
Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.
Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwe chifukwa ninji ndi marupiya atheka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka? Ndipo ndidziwa kuti lamulo lake lili moyo wosatha; chifukwa chake zimene ndilankhula, monga momwe Atate wanena ndi Ine, momwemo ndilankhula. Koma ananena ichi si chifukwa analikusamalira osauka, koma chifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoikidwamo.
Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.
Pakuti mwa iwo munalibe wosowa; pakuti onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nao malonda ake a izo adazigulitsa, nawaika pa mapazi a atumwi; ndipo anagawira yense monga kusowa kwake.
Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?
Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!
Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandire? Mwadzala kale, mwalemerera kale, mwachita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi muchitadi ufumu, kuti ifenso tikachite ufumu pamodzi ndi inu.
Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.
kuti m'chitsimikizo chachikulu cha chisautso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chao, ndi kusauka kwao, kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuolowa mtima kwao.
Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.
Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta. Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera. Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;
Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu; polemeretsedwa inu m'zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.
Tili ndi maomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake, chimene anatichulukitsira ife m'nzeru zonse, ndi chisamaliro.
Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.
kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;
Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo; kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane; nadzikundikire okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.
amene anatsanulira pa ife mochulukira, mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu; kuti poyesedwa olungama ndi chisomo cha Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa chiyembekezo cha moyo wosatha.
Pakuti munamva chifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.
ndipo mbale wolemera anyadire pamene atsitsidwa, pakuti adzapita monga duwa la udzu. Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m'mayendedwe ake.
Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu. Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m'dzina la Ambuye. Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo. Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro. Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire. Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye: ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye. Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake. Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwe mvula padziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi. Ndipo anapempheranso; ndipo m'mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake. Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake; Chuma chanu chaola ndi zovala zanu zajiwa ndi njenjete. azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa kunjira yake yosochera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzavundikira machimo aunyinji. Golide wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza.
Chifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndili nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa; ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m'moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.