Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 8:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Mbeu zogwera pa zitsamba zaminga zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, koma pambuyo pake nkhaŵa, kukondetsa chuma, ndiponso khumbo la zokondweretsa za moyo uno zimaŵalepheretsa, ndipo zipatso zao sizikhwima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Mbewu zimene zinagwa pakati pa minga zikuyimira anthu amene amamva mawu, koma akamayenda mʼnjira zawo amatsamwitsidwa ndi zodandaulitsa za moyo uno, chuma ndi zosangalatsa, ndipo iwo samakhwima.

Onani mutuwo Koperani




Luka 8:14
17 Mawu Ofanana  

Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso.


ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda chipatso.


Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.


Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;


Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka.


Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.


Ndipo zina zinagwa pakati pa minga; ndi mingayo inaphuka pamodzi nazo, nkuzitsamwitsa.


Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.


Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;


pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalamatiya.


Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe cha Khristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa