Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 6:2 - Buku Lopatulika

2 munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma ndi ulemu, mtima wake susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ichi ndi chabe ndi nthenda yoipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma ndi ulemu, mtima wake susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ichi ndi chabe ndi nthenda yoipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Mulungu kukulemeretsa, kukupatsa chuma ndi ulemu, osasoŵa kanthu kalikonse kamene ukukalakalaka, koma tsono osakupatsa mwai woti udyerere zinthuzo, wodyerera nkukhala munthu wachilendo. Zimenezi nzothetsa nzeru, ndipo ndi vuto lokhumudwitsa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mulungu amapereka chuma, zinthu ndi ulemu kwa munthu, kotero kuti munthuyo sasowa kanthu kalikonse kamene akukalakalaka, koma Mulungu samulola kuti adyerere zinthuzo, ndipo mʼmalo mwake amadyerera ndi mlendo. Izi ndi zopandapake, ndi zoyipa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 6:2
24 Mawu Ofanana  

Ndiponso zimene sunazipemphe adakupatsa, ndipo chuma ndi ulemu, kuti pakati pa mafumu sipadzakhala ina yolingana ndi iwe masiku ako onse.


Ndipo Yehova anakuza Solomoni kwakukulu pamaso pa Aisraele onse, nampatsa ulemerero wachifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Israele inali nao wotero.


Nafa atakalamba bwino, wochuluka masiku, zolemera, ndi ulemerero; ndi Solomoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ndipo Mulungu anati kwa Solomoni, Popeza chinali mumtima mwako ichi, osapempha chuma, akatundu, kapena ulemu, kapena moyo wa iwo akudana nawe, osapemphanso masiku ambiri; koma wadzipemphera nzeru ndi chidziwitso, kuti uweruze anthu anga amene ndakuika ukhale mfumu yao,


kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.


Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?


Kunenepa kwao kutuzulitsa maso ao, malingaliro a mitima yao asefukira.


Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.


Pali choipa chovuta ndachiona kunja kuno, ndicho, chuma chilikupweteka eni ake pochikundika;


Ichinso ndi choipa chowawa, chakuti adzangopita monse monga anadza; ndipo wodzisautsa chabe adzaona phindu lanji?


Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli.


Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lake ndi kukondwera ndi ntchito zake; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu.


Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona.


Cholowa chathu chasanduka cha alendo, ndi nyumba zathu za achilendo.


Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi chifumu;


Alendo anatha mphamvu yake osachidziwa iye; imvi zomwe zampakiza osachidziwa iye.


Mtundu wa anthu umene simuudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi ntchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;


Mlendo wokhala pakati panu adzakulirakulira inu, koma inu mudzacheperachepera.


Pomuka inu mudzafikira anthu okhazikika mtima ndi dziko lachitando; pakuti Mulungu walipereka m'dzanja lanu; pamenepo mposasowa kanthu kalikonse kali padziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa