Mlaliki 6 - Buku LopatulikaNgakhale Mulungu apatsa munthu zonse azikhumba koma mtima sukhuta nazo 1 Pali choipa ndachiona kunja kuno chifalikira mwa anthu, 2 munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma ndi ulemu, mtima wake susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ichi ndi chabe ndi nthenda yoipa. 3 Chinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zake ndi kuchuluka, koma mtima wake osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo; 4 pakuti ikudza mwachabe, nichoka mumdima, mdima nukwirira dzina lake. 5 Ngakhale dzuwa siliona ngakhale kulidziwa, imeneyi ipambana winayo kupuma; 6 akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita kumalo amodzi? 7 Ntchito zake zonse munthu angogwirira m'kamwa mwake, koma mtima wake sukhuta. 8 Pakuti wanzeru ali ndi chiyani choposa chitsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pamaso pa amoyo ali ndi chiyani? 9 Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima. 10 Chomwe chinalipo chatchedwa dzina lake kale, chidziwika kuti ndiye munthu; sangathe kulimbana ndi womposa mphamvu. 11 Pokhala zinthu zambiri zingochulukitsa zachabe, kodi anthu aona phindu lanji? 12 Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno? |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi