Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 6:10 - Buku Lopatulika

10 Chomwe chinalipo chatchedwa dzina lake kale, chidziwika kuti ndiye munthu; sangathe kulimbana ndi womposa mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Chomwe chinalipo chatchedwa dzina lake kale, chidziwika kuti ndiye munthu; sakhoza kulimbana ndi womposa mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Chilichonse chimene chilipo adachitchula kale dzina. Za m'mene munthu aliri nzodziŵika, nchomveka kuti sangathe kutsutsana ndi amene ali wamphamvu kupambana iyeyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Chilichonse chimene chilipo anachitchula kale dzina, za mmene munthu alili nʼzodziwika; sangathe kutsutsana ndi munthu amene ali wamphamvu kupambana iyeyo.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 6:10
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova Mulungu anaitana mwamunayo nati kwa iye, Uli kuti?


Mutsutsana ndi Iye chifukwa ninji? Popeza pa zake zonse sawulula chifukwa.


Kodi wodzudzulayo atsutsane ndi Wamphamvuyonse? Wochita makani ndi Mulungu ayankhe.


Pakuti sindiye munthu, monga ine, kuti ndimyankhe. Kuti tikomane mlandu.


Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa lakuthengo.


Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Chomwe chinaoneka, chilikuonekabe; ndi chomwe chidzaoneka chinachitidwa kale; Mulungu anasanthula zochitidwa kale.


Pokhala zinthu zambiri zingochulukitsa zachabe, kodi anthu aona phindu lanji?


Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amchokere; ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake, pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?


Kapena kodi tichititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa Iye?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa