Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 6:12 - Buku Lopatulika

12 Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ndani amadziŵa zomkomera munthu kwenikweni pa nthaŵi yochepa imene munthuyo ali ndi moyo? Moyo wake ndi wa masiku ochepa, ndi wopandapake, umangopitirira ngati mthunzi. Ndani angathe kumufotokozera munthuyo zimene zidzachitike pansi pano iyeyo atafa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Pakuti ndani amene amadziwa chomwe ndi chabwino pa moyo wa munthu, pakuti moyo wake ndi wa masiku ochepa ndi opandapake, umangopitira ngati mthunzi. Ndani amene angamufotokozere zimene zidzachitika pansi pano iye atapita?

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 6:12
28 Mawu Ofanana  

Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.


Atuluka ngati duwa, nafota; athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.


Ana ake aona ulemu osadziwa iye; napeputsidwa, koma osazindikira za iwo.


Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu, popeza masiku athu a padziko lapansi ndiwo ngati mthunzi;


Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali; ndipo ine ndauma ngati udzu.


Ndamuka ngati mthunzi womka m'tali; ndiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe.


Munthu akunga mpweya; masiku ake akunga mthunzi wopitirira.


Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa, ndinu wondigwirira cholandira changa.


Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m'chilungamo, ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka.


Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.


Atisankhira cholowa chathu, chokometsetsa cha Yakobo amene anamkonda.


Kumbukirani kuti nthawi yanga njapafupi; munalengeranji ana onse a anthu kwachabe?


Chitsiru chichulukitsanso mau; koma munthu sadziwa chimene chidzaoneka; ndipo ndani angamuuze chomwe chidzakhala m'tsogolo mwake?


Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.


Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m'ntchito yake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera kudzanja la Mulungu.


Ndinafuna mumtima mwanga kusangalatsa thupi langa ndi vinyo, mtima wanga ulikunditsogolera mwanzeru, ndi kugwira utsiru, kuti ndizindikire chabwinocho cha ana a anthu nchiyani chimene azichichita pansi pa thambo masiku onse a moyo wao.


M'mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi ntchito zake; pakuti gawo lake ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona chomwe chidzachitidwa atafa iyeyo?


Pokhala zinthu zambiri zingochulukitsa zachabe, kodi anthu aona phindu lanji?


Ndaona zonsezi masiku anga achabe; pali wolungama angofa m'chilungamo chake, ndipo pali woipa angokhalabe ndi moyo m'kuipa kwake.


koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ake ngati mthunzi; chifukwa saopa pamaso pa Mulungu.


pakuti sadziwa chimene chidzakhala; pakuti ndani angamuuze nthawi yakuti chidzachitidwa?


Chikondi chao ndi mdano wao ndi dumbo lao lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kalikonse kachitidwe pansi pano.


Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.


Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.


inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa