Mlaliki 6:3 - Buku Lopatulika3 Chinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zake ndi kuchuluka, koma mtima wake osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Chinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zake ndi kuchuluka, koma mtima wake osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Munthu ngakhale abale ana zana limodzi, nkukhala ndi moyo zaka zambiri, ngakhale zaka zakezo zichuluke chotani, ngati sakondwerera zinthu zabwino za pa moyo wake, potsiriza osalandira maliro aulemu, ndithu ine ndikuti munthuyo ngakhale mtayo womwe umpambana kwambiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Ngakhale munthu atabereka ana 100 ndi kukhala ndi moyo zaka zambiri; komatu ngakhale atakhala zaka zambiri chotani, ngati iye sangadyerere chuma chake ndi kuyikidwa mʼmanda mwaulemu, ine ndikuti mtayo umamuposa iyeyo. Onani mutuwo |
Ndipo Rehobowamu anakonda Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu koposa akazi ake onse, ndi akazi ake aang'ono (pakuti adatenga akazi khumi mphambu asanu ndi atatu, ndi akazi aang'ono makumi asanu ndi limodzi, nabala ana aamuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu, ndi ana aakazi makumi asanu ndi limodzi).