Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 9:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo Tiro adzadzimangira polimbikirapo, nadzakundika siliva ngati fumbi, ndi golide woyenga ngati thope la kubwalo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Tiro adzadzimangira polimbikirapo, nadzakundika siliva ngati fumbi, ndi golide woyenga ngati thope la kubwalo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tiro adadzimangira linga. Adaunjika siliva ngati dothi, adakundika golide ngati chifwilimbwiti cham'miseu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ndipo Turo anadzimangira linga; wadziwunjikira siliva ngati fumbi, ndi golide ngati zinyalala za mʼmisewu.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 9:3
16 Mawu Ofanana  

nafika ku linga la Tiro ndi kumizinda yonse ya Ahivi ndi ya Akanani; natulukira kumwera kwa Yuda ku Beereseba.


Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndi zotengera zonse za nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide yekhayekha, panalibe zasiliva, pakuti siliva anangoyesedwa opanda pake masiku onse a Solomoni.


Ndipo mfumu inachulukitsa siliva ngati miyala mu Yerusalemu, ndi mitengo yamikungudza anailinganiza ndi mikuyu ya m'madambo.


Ndipo utaye chuma chako kufumbi, ndi golide wa ku Ofiri ku miyala ya kumitsinje.


Chinkana akundika ndalama ngati fumbi, ndi kukonzeratu zovala ngati dothi;


kapena pamodzi ndi akalonga eni ake a golide, odzaza nyumba zao ndi siliva;


Iye watambasula dzanja lake panyanja, wagwedeza maufumu; Yehova walamulira Kanani za amalonda, kupasula malinga ake.


Ndani wapanga uphungu uno pa Tiro, mudzi umene upereka akorona, amalonda ake ali akalonga, ogulitsa ake ali olemekezeka padziko lapansi?


Ndipo adzalanda chuma chako ndi kufunkha malonda ako, nadzagwetsa malinga ako ndi kupasula nyumba zako zofunika, nadzaponya miyala yako, ndi mitengo yako, ndi fumbi lako, m'madzi.


Chuma chako, zako zogulana nazo malonda ako, amalinyero ako, ndi oongolera ako, amisiri ako, ndi ogulitsa malonda ako, ndi ankhondo ako onse okhala mwa iwe, pamodzi ndi msonkhano wonse uli pakati pa iwe, adzagwa m'kati mwa nyanja tsiku la kugwa kwako.


Pakutuluka malonda ako m'nyanja unadzaza mitundu yambiri ya anthu, unalemeretsa mafumu a padziko lapansi ndi chuma chako chochuluka ndi malonda ako.


Muja unathyoka ndi nyanja m'madzi akuya malonda ako ndi msonkhano wako wonse adagwa pakati pako.


Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Tiro, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukira pangano lachibale;


nazungulira malire kunka ku Rama, ndi kumzinda wa linga la Tiro; nazungulira malire kunka ku Hosa; ndi matulukiro ake anali kunyanja, kuchokera ku Mahalabu mpaka ku Akizibu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa