Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 9:4 - Buku Lopatulika

4 Taonani, Ambuye adzamlanda zake, nadzakantha mphamvu yake igwe m'manja; ndipo adzatha ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Taonani, Yehova adzamlanda zake, nadzakantha mphamvu yake igwe m'manja; ndipo adzatha ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Koma taimani, Chauta adzamlanda chuma chonsechi, adzachitaya m'nyanja, iyeyo adzapserera ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Taonani Ambuye adzamulanda chuma chakecho ndi kuwononga mphamvu zake mʼnyanja, ndipo adzapserera ndi moto.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 9:4
14 Mawu Ofanana  

Chuma cha uchimo sichithangata; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.


Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.


Iye watambasula dzanja lake panyanja, wagwedeza maufumu; Yehova walamulira Kanani za amalonda, kupasula malinga ake.


Ndipo adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kunena nawe, Watayika bwanji, ndiwe pokhala pa anthu a panyanja, mzinda womveka, unalimbika panyanja, uwo ndi okhalamo, amene anakhalitsa kuopsa kwao pa onse okhala momwemo!


Mwa kuchuluka kwa malonda ako anakudzaza m'kati mwako ndi chiwawa, ndipo unachimwa; chifukwa chake ndinakukankha kukuchotsa paphiri la Mulungu; ndipo ndinakuononga, kerubi wakuphimba iwe, kukuchotsa pakati pa miyala yamoto.


Mwa mphulupulu zako zochuluka ndi malonda ako osalungama waipsa malo ako opatulika; chifukwa chake ndatulutsa moto m'kati mwako wakunyeketsa iwe; ndipo ndakusandutsa mapulusa panthaka pamaso pa onse akuona.


Wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa kalonga wa Tiro, Atero Ambuye Yehova, Popeza mtima wako wadzikweza, nuti, Ine ndine Mulungu, ndikhala pa mpando wa Mulungu pakati pa nyanja, ungakhale uli munthu, wosati Mulungu, ungakhale waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu,


Adzakutsitsira kumanda, nudzafa mafedwe a ophedwa m'kati mwa nyanja.


ndipo ndidzagulitsa ana ako aamuna ndi aakazi m'dzanja la ana a Yuda; ndipo iwo adzawagulitsa kwa anthu a Seba, kwa anthu okhala kutali; pakuti Yehova wanena.


koma ndidzatumiza moto pa linga la Tiro, ndipo udzanyeketsa nyumba zake zachifumu.


Asikeloni adzachiona, nadzaopa; Gazanso, nadzanjenjemera kwambiri; ndi Ekeroni, pakuti chiyembekezo chake chachitidwa manyazi; ndipo mfumu idzataika ku Gaza, ndi Asikeloni adzasowa okhalamo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa