Zekariya 9:5 - Buku Lopatulika5 Asikeloni adzachiona, nadzaopa; Gazanso, nadzanjenjemera kwambiri; ndi Ekeroni, pakuti chiyembekezo chake chachitidwa manyazi; ndipo mfumu idzataika ku Gaza, ndi Asikeloni adzasowa okhalamo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Asikeloni adzachiona, nadzaopa; Gazanso, nadzanjenjemera kwambiri; ndi Ekeroni, pakuti chiyembekezo chake chachitidwa manyazi; ndipo mfumu idzataika ku Gaza, ndi Asikeloni adzasowa okhalamo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Mzinda wa Asikeloni nawonso udzaziwona zimenezo, nkuchita mantha. Gaza adzakhwinyata ndi mantha, Ekeroninso chimodzimodzi, chifukwa zimene ankayembekeza zidzasokonezeka. Mfumu ya ku Gaza idzachotsedwa, ku Asikeloni kudzakhala kopanda anthu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Mzinda wa Asikeloni udzaona zimenezi, nʼkuchita mantha; Gaza adzanjenjemera ndi ululu, chimodzimodzinso Ekroni, chifukwa chiyembekezo chake chidzatheratu. Mfumu ya ku Gaza idzaphedwa ndipo Asikeloni adzakhala opanda anthu. Onani mutuwo |