Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


118 Mau a m'Baibulo Oletsa Kuweruza

118 Mau a m'Baibulo Oletsa Kuweruza

Tanthauzo la kuweruza m'Baibulo ndi kupanga chigamulo kapena maganizo pa chinthu kapena munthu wina. Tikamadzipanga oweluza ena, timadzikweza tokha pamwamba pa ena, zomwe sizikugwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.

Koma si kuweruza konse koipa; chomwe chili choipa ndi chinyengo. “Nanga iwe, uziona bwanji kachitsotso kali m’diso la m’bale wako, koma suzindira mtanda uli m’diso lako mwini? Kapena, unganene bwanji kwa m’bale wako, ‘Ndikulole ndikuchotse kachitsotsoko m’diso lako,’ pamene mtanda uli m’diso lako mwini? Wonyenga iwe! Choyamba chotsa mtanda m’diso lako mwini, ndipo pamenepo udzatha kuona bwino kuti uchotse kachitsotso m’diso la m’bale wako.” (Mateyu 7:3-5). Yesu amatsutsa chinyengo, akutiyeni tiyang'ane kaye mtima wathu tisanayambe kuweruza ena. Tifunikira kuchotsa mtanda m'maso mwathu tisanayambe kuchotsa kachitsotso m'maso mwa mnzathu.

Kodi njira yoyenera yoweruzira ndi iti? Choyamba, chilungamo n'chofunika kwambiri. Yesu anatiphunzitsa kuti: “Musamaweruze anthu potengera maonekedwe awo, koma weruzani mwachilungamo.” (Yohane 7:24).

Chachiwiri, ngati tikuweruza ena, tizichita zimenezi mwachikondi, popanda chinyengo, ndi kuwaitana kuti alape.




Mateyu 7:1-5

Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi? Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye? Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri. Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka. Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso. Inde chomwecho pa zipatso zao mudzawazindikira iwo. Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenere mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziweni inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika. Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwe; chifukwa inakhazikika pathanthwepo. Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu. Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake: pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembi ao. Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira? Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli. Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m'diso la mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:31

Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitirani inu, muwachitire iwo motero inu momwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 11:3

ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova, ndipo sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:1-2

Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi? Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye? Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri. Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka. Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:37

Ndipo musawatsutsa, ndipo simudzamatsutsidwa. Khululukani, ndipo mudzakhululukidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:16

Chifukwa chake munthu aliyense asakuweruzeni inu m'chakudya, kapena chakumwa, kapena m'kunena tsiku la chikondwerero, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena la Sabata;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:10

Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzaimirira kumpando wakuweruza wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:1-4

Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe. Pakuti aliyense amene angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse. Pakuti Iye wakuti, Usachite chigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo. Lankhulani motero, ndipo chitani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu. Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro. Chipindulo chake nchiyani, abale anga, munthu akanena, Ndili nacho chikhulupiriro, koma alibe ntchito? Kodi chikhulupirirocho chikhoza kumpulumutsa? Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, ndi kusowa chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake nchiyani? Momwemonso chikhulupiriro, chikapanda kukhala nacho ntchito, chikhala chakufa m'kati mwakemo. Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndili nazo ntchito; undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m'ntchito zanga. Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira. Pakuti akalowa m'sunagoge mwanu munthu wovala mphete yagolide, ndi chovala chokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi chovala chodetsa; Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe? Abrahamu kholo lathu, sanayesedwe wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake Isaki nsembe paguwa la nsembe? Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro; ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu. Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha. Ndipo momwemonso sanayesedwe wolungama Rahabu mkazi wa damayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira ina? Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa. ndipo mukapenyerera iye wovala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, imauko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga; kodi simunasiyanitse mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:11-12

Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza. Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:1-3

Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo. koma ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino, kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki; pakuti Mulungu alibe tsankho. Pakuti onse amene anachimwa opanda lamulo adzaonongeka opanda lamulo; ndi onse amene anachimwa podziwa lamulo adzaweruzidwa ndi lamulo; pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzayesedwa olungama. Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo; popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao, ndipo chikumbumtima chao chichitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana; tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Khristu Yesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino. Koma ngati iwe unenedwa Myuda, nukhazikika palamulo, nudzitamandira pa Mulungu, nudziwa chifuniro chake, nuvomereza zinthu zoposa, utaphunzitsidwa m'chilamulo, nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima, Ndipo tidziwa kuti kuweruza kwa Mulungu kuli koona pa iwo akuchita zotere. wolangiza wa opanda nzeru, mphunzitsi wa tiana, wakukhala m'chilamulo ndi chionekedwe cha nzeru ndi cha choonadi; ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha? Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za mu Kachisi kodi? Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m'chilamulo? Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa. Pakuti inde mdulidwe uli wabwino, ngati iwe umachita lamulo; koma ngati uli wolakwira lamulo, mdulidwe wako wasanduka kusadulidwa. Chifukwa chake ngati wosadulidwa asunga zoikika za chilamulo, kodi kusadulidwa kwake sikudzayesedwa ngati mdulidwe? Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa chibadwidwe, ngati kukwanira chilamulo, kodi sikudzatsutsa iwe, amene uli nao malembo ndi mdulidwe womwe, ndiwe wolakwira lamulo? Pakuti siali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m'thupimo; koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m'malembo ai; kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu, koma kwa Mulungu. Ndipo uganiza kodi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akuchita zotere, ndipo uzichitanso iwe mwini, kuti udzapulumuka pa mlandu wa Mulungu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:37-42

Ndipo musawatsutsa, ndipo simudzamatsutsidwa. Khululukani, ndipo mudzakhululukidwa. Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu. Ndipo Iye ananenanso nao fanizo, Kodi munthu wakhungu angathe kutsogolera mnzake wakhungu? Kodi sadzagwa onse awiri m'mbuna? kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha? Wophunzira saposa mphunzitsi wake; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wake. Ndipo uyang'aniranji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda wa m'diso la iwe mwini suuzindikira? Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndichotse kachitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m'diso la mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:12-13

Pakuti nditani nao akunja kukaweruza iwo? Kodi amene ali m'katimo simuwaweruze ndi inu, koma akunja awaweruza Mulungu? Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:3-5

Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira? Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli. Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m'diso la mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:1-6

Kodi akhoza wina wa inu, pamene ali nao mlandu pa mnzake, kupita kukaweruzidwa kwa osalungama, osati kwa oyera mtima? kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa nacho chimodzi. Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi; koma Mulungu anaukitsa Ambuye, ndiponso adzaukitsa ife mwa mphamvu yake. Kodi simudziwa kuti matupi anu ali ziwalo za Khristu? Chifukwa chake ndidzatenga ziwalo za Khristu kodi, ndi kuziyesa ziwalo za mkazi wachiwerewere? Msatero iai. Kapena simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi wachiwerewere ali thupi limodzi? Pakuti awiriwo, ati, adzakhala thupi limodzi. Koma iye wophatikidwa ndi Ambuye ali mzimu umodzi. Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha. Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa? Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu. Kodi simudziwa kuti tidzaweruza angelo? Koposa kotani nanga zinthu za moyo uno? Chifukwa chake, ngati muli nayo milandu ya zinthu za moyo uno, kodi muweruzitsa iwo amene ayesedwa achabe mu Mpingo? Ndinena ichi kukuchititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe mmodzi wanzeru, amene adzakhoza kuweruza pa abale, koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa osakhulupirira?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:1

Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:29

Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:5

Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m'diso la mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:7

Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe Iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda tchimo, ayambe kumponya mwala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:14-15

Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba. Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:26

Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:14

Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:17

Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:15

Koma iye amene ali wauzimu ayesa zonse, koma iye yekha sayesedwa ndi mmodzi yense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 7:24

Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani chiweruziro cholungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:15-16

Inu muweruza monga mwa thupi; Ine sindiweruza munthu. Ndipo ngati ndiweruza Ine, chiweruziro changa chili choona; pakuti sindili pa ndekha, koma Ine ndi Atate amene anandituma Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:41-42

Ndipo uyang'aniranji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda wa m'diso la iwe mwini suuzindikira? Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndichotse kachitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m'diso la mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 16:18-20

Mudziikire oweruza ndi akapitao m'midzi yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, monga mwa mafuko anu; ndipo aweruze anthu ndi chiweruzo cholungama. Musamapotoza chiweruzo, musamasamalira munthu, kapena kulandira chokometsera mlandu; popeza chokometsera mlandu chidetsa maso a anzeru, ndi kuipisa mau a olungama. Ndipo muziphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, ya nkhosa ndi ya ng'ombe, m'malo amene Yehova adzasankha kukhalitsamo dzina lake. Chilungamo, chilungamo ndicho muzichitsata, kuti mukhale ndi moyo ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:6-7

Usakhotetsa mlandu wa mnzako waumphawi. Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosachimwa ndi wolungama; pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 1:16-17

Ndipo ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wake, ndi mlendo wokhala naye. Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akulu muwamvere chimodzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza chiweruzo ncha Mulungu; ndipo mlandu ukakukanikani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:7

Odala ali akuchitira chifundo; chifukwa adzalandira chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1

Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:20

Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sangathe kukonda Mulungu amene sanamuone.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:2

Njira zonse za munthu zilungama pamaso pake; koma Yehova ayesa mitima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:13

Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa panjira ya mbale wake, kapena chomphunthwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:13

Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:36-37

Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza. Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:23-24

Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:12

Pali mbadwo wodziyesa oyera, koma osasamba litsiro lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:13

kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:30

pakuti timdziwa Iye amene anati, Kubwezera chilango nkwanga, Ine ndidzabwezera. Ndiponso, Ambuye adzaweruza anthu ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:1

Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:20

Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:2

Njira zonse za munthu ziyera pamaso pake; koma Yehova ayesa mizimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:5

Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:7

Chifukwa chake mulandirane wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:11

Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:4

Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu; kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:23

pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:10

Pakuti Mwana wa Munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:21-22

Pamenepo Petro anadza, nati kwa Iye, Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? Kufikira kasanu ndi kawiri kodi? Yesu ananena kwa iye, Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi asanu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:15

Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Khristu Yesu anadza kudziko lapansi kupulumutsa ochimwa; wa iwowa ine ndine woposa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:12-13

Ndipo m'mene Yesu anamva anati, Olimba safuna sing'anga ai, koma odwala. Koma mukani muphunzire nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadze kudzaitana olungama, koma ochimwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:3

Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:15

Njira ya chitsiru njolungama pamaso pakepake; koma wanzeru amamvera uphungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 130:3-4

Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye? Koma kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:3

Pakuti ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:16-17

Chifukwa chake munthu aliyense asakuweruzeni inu m'chakudya, kapena chakumwa, kapena m'kunena tsiku la chikondwerero, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena la Sabata; ndizo mthunzi wa zilinkudzazo; koma thupi ndi la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:46-48

Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho? Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okhaokha, muchitanji choposa ena? Kodi angakhale anthu akunja sachita chomwecho? Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:35

Koma takondanani nao adani anu, ndi kuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:6

Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 43:1

Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:19

Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:1

Musaweruze, kuti mungaweruzidwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:6

Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:8

Usatuluke mwansontho kukalimbana, ungalephere pa kutha kwake, atakuchititsa mnzako manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:8

Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:10

Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m'thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 26:2

Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe; yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:15

koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:20

bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzaizima, kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:12

Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang'anire kuti angagwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:32

Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:2

Wina akutume, si m'kamwa mwako ai; mlendo, si milomo ya iwe wekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:17

Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:24-25

Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza, wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:1-2

Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama. Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti; inde, udzayang'anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nao mtendere wochuluka. Woipa apangira chiwembu wolungama, namkukutira mano. Ambuye adzamseka, popeza apenya kuti tsiku lake likudza. Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao; alikhe ozunzika ndi aumphawi, aphe amene ali oongoka m'njira. Lupanga lao lidzalowa m'mtima mwao momwe, ndipo mauta ao adzathyoledwa. Zochepa zake za wolungama zikoma koposa kuchuluka kwao kwa oipa ambiri. Pakuti manja a oipa adzathyoledwa, koma Yehova achirikiza olungama. Yehova adziwa masiku a anthu angwiro; ndipo cholowa chao chidzakhala chosatha. Sadzachita manyazi m'nyengo yoipa, ndipo m'masiku a njala adzakhuta. Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauwisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:12

Kuchita mphulupulu kunyansa mafumu; pakuti mpando wao wakhazikika ndi chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:14

Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3-4

musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine. munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:104

Malangizo anu andizindikiritsa; chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:7

Kodi si ndiko kupatsa chakudya chako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? Pakuona wamaliseche kuti umveke, ndi kuti usadzibisire wekha a chibale chako?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:17

Woyamba kudzinenera ayang'anika wolungama; koma mnzake afika namuululitsa zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 3:17

Ndinati mumtima wanga, Mulungu adzaweruza wolungama ndi woipa; pakuti pamenepo pali mphindi ya zofuna zonse ndi ntchito zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:9

Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12-13

Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:4

Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:33-34

Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo, nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:23

Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:19-20

Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima. Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu; Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:50

Ndipo Yesu anati kwa iye, Mnzanga, wafikiranji iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namgwira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:13

Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:4

Mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:16

Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:5

Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:8

Tikati kuti tilibe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:15-16

Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:59

Ndinaganizira njira zanga, ndipo ndinabweza mapazi anga atsate mboni zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:5

sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:10-11

Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pachakudya m'nyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. Ndipo Afarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:20

Kodi uona munthu wansontho m'mau ake? Ngakhale chitsiru chidzachenjera, koma ameneyo ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:1

Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Khristu wolungama;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13

Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:18

Ndikadasekera zopanda pake m'mtima mwanga, Ambuye sakadamvera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:12

Udani upikisanitsa; koma chikondi chikwirira zolakwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:12

Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:7

Koma mukadadziwa nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; simukadaweruza olakwa iwo osachimwa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:1-2

Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake. Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; ndipo anthu onse amtamande. Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Yese, ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera. Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera. Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzake. Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, chifukwa cha chisomo chapatsidwa kwa ine ndi Mulungu, kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera. Chifukwa chake ndili nacho chodzitamandira cha mu Khristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu. Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito, mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu; Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:14

Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:3-5

Koma kwa ine kuli kanthu kakang'ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha. Pakuti sindidziwa kanthu kakundipalamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye. Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:3

Kuchita chilungamo ndi chiweruzo kupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:155

Chipulumutso chitalikira oipa; popeza safuna malemba anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:1-2

Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala padzanja lamanja la Mulungu. ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye; pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse. Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu. Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika. Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu. Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye. Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye. Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo. Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Mulungu ndi wokhulupirika ndipo chikondi chake chachikulu chimakhala kosatha, nthawi zonse wawonetsa chifundo chake kwa ana ake onse ndipo malonjezo ake sazengereza kuwakwaniritsa. Ndimalemekeza dzina la Wamphamvuyonse ndipo moyo wanga umamutambasira, pamaso pake pali chisangalalo chokwanira, ndimalowa molimba mtima m'malo anu opatulika ndipo ndimagwadira mapazi anu kuti ndikupatseni ulemerero wonse, inu nokha Ambuye wanga ndinu woyenera, chifukwa ndinu wangwiro ndi wolungama pa zonse zomwe mumachita, chifukwa njira zanu ndi zolungama ndipo mulibe kuipa kapena chinyengo, ndimapembedza iye amene wakhala pampando wachifumu, maso ake ali pa chilengedwe chonse ndipo iye ndiye woweruza dziko lonse lapansi, iye yekha ndiye angaweruze komanso kupulumutsa, palibe wina wofanana ndi Mulungu wanga, pamaso pake mdima umathawira, iye ndi Yehova woopsa ndi wosagonjetseka, ndimakhulupirira ziweruzo zanu zolungama, inu ndinu wanzeru Ambuye ndipo palibe wina woposa inu kukhala woweruza padziko lapansi, landirani ulemerero ndipo ulemu wonse ukhale kwa inu, m'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa