Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 7:20 - Buku Lopatulika

20 Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Ndithudi, pa dziko lapansi palibe munthu amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa konse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Palibe munthu wolungama pa dziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha ndipo sachimwa.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 7:20
16 Mawu Ofanana  

Akachimwira Inu, popeza palibe munthu wosachimwa, ndipo mukakwiya nao ndi kuwapereka kwa adani, kuti iwo awatenge ndende kunka nao ku dziko la adani, ngati kutali kapena kufupi,


Akachimwira Inu (pakuti palibe munthu wosachimwa), nimukakwiya nao, ndi kuwapereka kwa adani, kuti awatenge andende kunka nao ku dziko lakutali, kapena lapafupi;


Taonani, ndidzakuyankhani m'mene muli mosalungama; pakuti Mulungu ndiye wamkulu woposa munthu.


Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye?


Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino.


Anapatuka onse; pamodzi anavunda mtima; palibe wakuchita bwino ndi mmodzi yense.


Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu; pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense.


Ndani anganene, Ndasambitsa mtima wanga, ndayera opanda tchimo?


Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.


Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse zili ngati chovala chodetsedwa; ndipo ife tonse tifota monga tsamba, ndi zoipa zathu zitiuluza monga mphepo.


wansembe aziona; ndipo taonani ngati zikanga zili pa khungu la thupi lao zikhala zotuwatuwa; ndilo thuza labuka pakhungu; ndiye woyera.


pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu;


Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.


Pamenepo Yonatani anauka pagome wolunda ndithu, osadya kanthu tsiku lachiwiri la mwezi, pakuti mtima wake unali ndi chisoni chifukwa cha Davide, popeza atate wake anamchititsa manyazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa