Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yakobo 2:13 - Buku Lopatulika

13 Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachita chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Paja munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso Mulungu adzamuweruza mopanda chifundo. Koma wochita chifundo alibe chifukwa choopera chiweruzo cha Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 chifukwa munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso adzaweruzidwa mopanda chifundo. Chifundo chimapambana pa chiweruzo.

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 2:13
26 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo anati wina ndi mnzake, Tachimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kuvutidwa kwa mtima wake, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira.


Mundimvere tsono, bwezani andende a abale anu; pakuti mkwiyo waukali wa Yehova uli pa inu.


Pa wachifundo mukhala wachifundo; pa munthu wangwiro mukhala wangwiro.


Chifundo ndi choonadi zakomanizana; chilungamo ndi mtendere zapsompsonana.


Wotseka makutu ake polira waumphawi, nayenso adzalira koma osamvedwa.


Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake, ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.


Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.


koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.


Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?


Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.


Odala ali akuchitira chifundo; chifukwa adzalandira chifundo.


Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.


Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.


Ndipo musawatsutsa, ndipo simudzamatsutsidwa. Khululukani, ndipo mudzakhululukidwa.


Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.


Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.


Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko.


Pa mapazi ake anabzong'onyoka, anagwa, anagona; pa mapazi ake anabzong'onyoka, anagwa; pobzong'onyokapo, pamenepo wagwa wafa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa