Ndipo Davide ananyamuka, namuka nao anthu onse anali naye, nachokera ku Baale-Yuda natengako likasa la Mulungu, limene amatchula nalo Dzinalo, Dzina la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa Akerubi.
Masalimo 99:1 - Buku Lopatulika Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere; Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere; Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta ndiye mfumu, mitundu ya anthu injenjemere. Wakhala pa akerubi ngati pa mpando wake wachifumu. Dziko lapansi ligwedezeke! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova akulamulira, mitundu ya anthu injenjemere; Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi, dziko lapansi ligwedezeke. |
Ndipo Davide ananyamuka, namuka nao anthu onse anali naye, nachokera ku Baale-Yuda natengako likasa la Mulungu, limene amatchula nalo Dzinalo, Dzina la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa Akerubi.
Njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi, dziko lokhalamo anthu lomwe lakhazikika, kuti silingagwedezeke.
Mbusa wa Israele, tcherani khutu; inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; inu wokhala pa akerubi, walitsani.
Utsani chamuna chanu pamaso pa Efuremu ndi Benjamini ndi Manase, ndipo mutidzere kutipulumutsa.
Sadziwa, ndipo sazindikira; amayendayenda mumdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.
Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu; wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno; dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.
Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.
Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa, njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi.
Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndili pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israele.
Yehova wasakaniza mzimu wa kusaweruzika pakati pake; ndipo iwo asocheretsa Ejipito m'ntchito zake zonse, monga mwamuna woledzera ayenda punzipunzi posanza pake.
Dziko lapansi linthunthumira ndi phokoso la kugwa kwao; pali mfuu, phokoso lake limveka pa Nyanja Yofiira.
Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.
Dziko lapansi linthunthumira, pa phokoso la kugwidwa kwa Babiloni, ndipo mfuu wamveka mwa amitundu.
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wachifumu wanga, mpoponda kumapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israele kosatha; ndi nyumba ya Israele siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa chigololo chao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,
Pamenepo anati, Munthu wa fuko lomveka ananka kudziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako.
Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.
Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.
Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;
nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu.
Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.
Ndipo kumwamba kudachoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zinatunsidwa kuchoka m'malo mwao.