Masalimo 93 - Buku LopatulikaUfumu wa Mulungu ndiwo wa ulemerero, mphamvu, ndi chiyero 1 Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu; wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno; dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka. 2 Mpando wachifumu wanu ukhazikika kuyambira kale lija; Inu ndinu wosayambira ndi kale lomwe. 3 Mitsinje ikweza, Yehova, mitsinje ikweza mkokomo wao; mitsinje ikweza mafunde ao. 4 Yehova Wam'mwamba ndiye wamphamvu, wakuposa mkokomo wa madzi ambiri, ndi mafunde olimba a nyanja. 5 Mboni zanu zivomerezeka ndithu; chiyero chiyenera nyumba yanu, Yehova, kunthawi za muyaya. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi